Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 149:1-9

149  Tamandani Ya, anthu inu!+ Imbirani Yehova nyimbo yatsopano,+ Muimbireni nyimbo zomutamanda mu mpingo wa anthu ake okhulupirika.+   Isiraeli asangalale ndi Womupanga Wamkulu,+ Ana a Ziyoni akondwere ndi Mfumu yawo.+   Atamande dzina lake mwa kuvina.+ Amuimbire nyimbo zomutamanda ndi maseche ndi zeze,+   Pakuti Yehova amasangalala ndi anthu ake.+ Iye amakongoletsa anthu ofatsa ndi chipulumutso.+   Anthu okhulupirika akondwere mu ulemerero. Iwo aimbe mosangalala pamabedi awo.+   Pakamwa pawo patuluke nyimbo zotamanda Mulungu,+ Ndipo lupanga lakuthwa konsekonse likhale m’manja mwawo,+   Kuti abwezere anthu a mitundu ina,+ Ndi kudzudzula mitundu ya anthu,+   Ndiponso kuti amange mafumu awo maunyolo,+ Ndi kumanga anthu awo olemekezeka m’matangadza achitsulo.   Kuti awaweruze motsatira chigamulo cholembedwa.+ Ulemerero umenewu ndi wa anthu onse okhulupirika a Mulungu.+ Tamandani Ya, anthu inu!+

Mawu a M'munsi