Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 148:1-14

148  Tamandani Ya, anthu inu!+ Tamandani Yehova inu okhala kumwamba.+ Mutamandeni inu okhala m’mwamba.+   Mutamandeni, inu angelo ake onse.+ Mutamandeni, inu khamu lake lonse.+   Mutamandeni, inu dzuwa ndi mwezi.+ Mutamandeni, inu nyenyezi zonse zowala.+   Mutamandeni, inu kumwamba kwa m’mwambamwamba,+ Ndi inunso madzi okhala pamwamba pa miyamba.+   Zonsezi zitamande dzina la Yehova,+ Pakuti iye analamula ndipo zinalengedwa.+   Amazichititsa kukhalapobe kwamuyaya, ngakhalenso mpaka kalekale.+ Iye wazikhazikitsira lamulo, ndipo silidzatha.+   Tamandani Yehova, inu okhala padziko lapansi,+ Inu zilombo za m’nyanja ndi inu nonse madzi akuya,+   Inu moto ndi matalala, chipale chofewa ndi utsi wakuda bii,+ Iwe mphepo yamkuntho yokwaniritsa mawu ake.+   Mutamandeni inu mapiri ndi inu nonse zitunda,+ Inu mitengo ya zipatso ndi inu nonse mitengo ya mkungudza.+ 10  Inu nyama zakutchire ndi inu nonse nyama zoweta,+ Inu zinthu zokwawa ndi mbalame zamapiko.+ 11  Mutamandeni inu mafumu a padziko lapansi+ ndi inu nonse mitundu ya anthu, Inunso akalonga+ ndi inu nonse oweruza a padziko lapansi,+ 12  Inu anyamata+ ndi inunso anamwali,+ Inu okalamba+ pamodzi ndi ana.+ 13  Onse, anthu ndi nyama, atamande dzina la Yehova,+ Pakuti dzina lake lokhalo lili pamwamba posafikirika.+ Ulemerero wake uli pamwamba kuposa dziko lapansi ndi kumwamba.+ 14  Iye adzakweza nyanga* ya anthu ake.+ Adzachititsa kuti anthu ake onse okhulupirika atamandike,+ Amene ndi ana a Isiraeli, anthu amene ali pafupi ndi iye.+ Tamandani Ya, anthu inu!+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa 1Sa 2:1.