Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 147:1-20

147  Tamandani Ya, anthu inu,+Pakuti kuimbira Mulungu wathu nyimbo zomutamanda n’kwabwino,+Ndipo n’kosangalatsa. Kumutamanda n’koyenera.+   Yehova akumanga Yerusalemu.+Anthu okhala mu Isiraeli amene anabalalika akuwasonkhanitsanso pamodzi.   Iye amachiritsa+ anthu osweka mtima,+Ndipo amamanga zilonda zawo zopweteka.+   Amawerenga nyenyezi zonse,Ndipo zonsezo amazitchula mayina ake.+   Ambuye wathu ndi wamkulu ndipo ali ndi mphamvu zochuluka.Nzeru zake zilibe malire.+   Yehova amathandiza anthu ofatsa,Koma anthu oipa amawagwetsera pansi.+   Imbirani Yehova molandizana mawu nyimbo zomuyamikira anthu inu.+Imbirani Mulungu wathu nyimbo zomutamanda ndi zeze.+   Muimbireni Iye amene amaphimba mapiri ndi mitambo,Amene amakonza mvula kuti igwe padziko lapansi,+Amenenso amameretsa udzu wobiriwira m’mapiri.+   Iye amapatsa zilombo chakudya chawo,+Amapatsanso ana a makwangwala chakudya chimene amalirira.+ 10  Iye sadalira mphamvu za hatchi,+Kapena liwiro la miyendo ya munthu. 11  Yehova amasangalala ndi anthu amene amamuopa,+Amene amayembekezera kukoma mtima kwake kosatha.+ 12  Yamika Yehova,+ iwe Yerusalemu.Tamanda Mulungu wako, iwe Ziyoni.+ 13  Pakuti walimbitsa mipiringidzo ya zipata zako.Wadalitsa ana ako amene ali mwa iwe.+ 14  Iye akukhazikitsa mtendere m’dziko lako.Ndipo akupitirizabe kukukhutiritsa ndi tirigu wabwino koposa. 15  Amatumiza mawu ake padziko lapansi,+Ndipo mawu akewo amathamanga kwambiri. 16  Iye amapereka chipale chofewa kuti chikhale ngati ubweya wa nkhosa.+Amamwaza mame oundana ngati kuti ndi phulusa.+ 17  Amaponya madzi oundana ngati nyenyeswa za chakudya.Ndani angaime m’chisanu chake?+ 18  Amatumiza mawu ake+ ndi kusungunula madzi oundanawo.Amachititsa mphepo yake kuwomba,+Ndipo madzi amayenda. 19  Amauza Yakobo mawu ake,Ndipo amauza Isiraeli malangizo ake ndi zigamulo zake. 20  Sanachite zimenezi ndi mtundu wina uliwonse,Ndipo mitundu inayo sikudziwa zigamulo zake.Tamandani Ya, anthu inu!+

Mawu a M'munsi