Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 146:1-10

146  Tamandani Ya, anthu inu!+ Iwe moyo wanga, tamanda Yehova.+   Ndidzatamanda Yehova pamene ndili moyo.+ Ndidzaimbira Mulungu wanga nyimbo zomutamanda kwa moyo wanga wonse.+   Musamakhulupirire anthu olemekezeka,+ Kapena mwana wa munthu wina aliyense wochokera kufumbi amene alibe chipulumutso.+   Mzimu* wake umachoka,+ ndipo iye amabwerera kunthaka.+ Pa tsiku limenelo zonse zimene anali kuganiza zimatheratu.+   Wodala ndi munthu amene thandizo lake limachokera kwa Mulungu wa Yakobo,+ Amene chiyembekezo chake chili mwa Yehova Mulungu wake,+   Wopanga kumwamba ndi dziko lapansi,+ Nyanja ndi zonse zili mmenemo.+ Wosunga choonadi mpaka kalekale.+   Iye ndi Woperekera chiweruzo anthu ochitiridwa chinyengo,+ Wopereka chakudya kwa anthu anjala.+ Yehova amamasula anthu omangidwa.+   Yehova amatsegula maso a anthu akhungu.+ Yehova amaweramutsa anthu owerama chifukwa cha masautso.+ Yehova amakonda anthu olungama.+   Yehova amayang’anira alendo okhala m’dziko la eni.+ Amathandiza mwana wamasiye* ndi mkazi wamasiye.+ Koma njira+ ya anthu oipa amaichititsa kukhala yovuta kuyendamo.+ 10  Yehova adzakhala mfumu mpaka kalekale,+ Mulungu wako, iwe Ziyoni, adzakhala mfumu ku mibadwomibadwo.+ Tamandani Ya, anthu inu!+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 4.
Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”