Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 145:1-21

Nyimbo yotamanda Mulungu. Salimo la Davide. א [ʼAʹleph] 145  Ndidzakukwezani, inu Mfumu ndi Mulungu wanga,+ Ndipo ndidzatamanda dzina lanu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+ ב [Behth]   Ndidzakutamandani tsiku lonse.+ Ndidzatamanda dzina lanu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+ ג [Giʹmel]   Yehova ndi wamkulu ndi woyenera kutamandidwa kwambiri,+ Ndipo ukulu wake ndi wosasanthulika.+ ד [Daʹleth]   Anthu adzatamanda ntchito zanu ku mibadwomibadwo,+ Ndipo adzasimba za zochita zanu zamphamvu.+ ה [Heʼ]   Ndidzasinkhasinkha za ulemerero wanu waukulu+ Ndi nkhani zokhudza ntchito zanu zodabwitsa.+ ו [Waw]   Anthu adzanena za zochita zanu zamphamvu ndi zochititsa mantha.+ Ndipo ine ndidzalengeza za ukulu wanu.+ ז [Zaʹyin]   Iwo adzalankhula mosefukira za kuchuluka kwa ubwino wanu,+ Ndipo adzafuula mokondwera chifukwa cha chilungamo chanu.+ ח [Chehth]   Yehova ndi wachisomo ndi wachifundo,+ Wosakwiya msanga ndi wosonyeza kukoma mtima kosatha komanso kwakukulu.+ ט [Tehth]   Yehova amakomera mtima aliyense,+ Ndipo ntchito zake zonse amazichitira chifundo.+ י [Yohdh] 10  Ntchito zanu zonse zidzakutamandani, inu Yehova,+ Ndipo okhulupirika anu adzakutamandani.+ כ [Kaph] 11  Iwo adzanena za ulemerero wa ufumu wanu.+ Ndi kulankhula za mphamvu zanu,+ ל [Laʹmedh] 12  Kuti ana a anthu adziwe za ntchito zanu zamphamvu+ Ndi kukula kwa ulemerero wa ufumu wanu.+ מ [Mem] 13  Ufumu wanu ndi ufumu umene udzakhalapobe mpaka kalekale.+ Ulamuliro wanu udzakhalapobe ku mibadwo yonse.+ ס [Saʹmekh] 14  Yehova amachirikiza amene ali pafupi kugwa,+ Ndipo amaweramutsa onse amene awerama chifukwa cha masautso.+ ע [ʽAʹyin] 15  Zolengedwa zonse zimayang’ana kwa inu mwachiyembekezo,+ Ndipo mumazipatsa chakudya pa nyengo yake.+ פ [Peʼ] 16  Mumatambasula dzanja lanu+ Ndi kukhutiritsa zokhumba za chamoyo chilichonse.+ צ [Tsa·dhehʹ] 17  Yehova ndi wolungama m’njira zake zonse,+ Ndipo ndi wokhulupirika m’ntchito zake zonse.+ ק [Qohph] 18  Yehova ali pafupi ndi onse oitanira pa iye.+ Iye ali pafupi ndi onse amene amamuitana m’choonadi,+ ר [Rehsh] 19  Ndipo anthu amene amamuopa adzawachitira zokhumba zawo,+ Adzamva kufuula kwawo kopempha thandizo  ndipo adzawapulumutsa.+ ש [Shin] 20  Yehova amayang’anira onse omukonda,+ Koma oipa onse adzawafafaniza.+ ת [Taw] 21  Pakamwa panga padzalankhula zotamanda Yehova,+ Ndipo anthu onse atamande dzina lake loyera mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+

Mawu a M'munsi