Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 144:1-15

Salimo la Davide. 144  Atamandike Yehova Thanthwe langa,Amene akuphunzitsa manja anga kumenya nkhondo,Amenenso akuphunzitsa zala zanga kumenyana ndi adani anga.   Iye amandisonyeza kukoma mtima kwake kosatha ndipo ndiye malo anga achitetezo,Malo anga okwezeka ndi Wopereka chipulumutso,Chishango changa ndi malo anga othawirako.+Iye amandigonjetsera mitundu ya anthu.+   Inu Yehova, munthu ndani kuti mumuganizire?+Kodi mwana wa munthu wochokera kufumbi+ ndani kuti mumuwerengere?   Munthu amafanana ndi mpweya wotuluka m’mphuno.+Masiku ake ali ngati mthunzi wongodutsa.   Inu Yehova, weramitsani kumwamba kuti mutsike.+Khudzani mapiri kuti afuke utsi.   Ng’animitsani mphezi kuti muwabalalitse.Tumizani mivi yanu kuti muwasokoneze.   Tambasulani manja anu kuchokera kumwamba.Ndimasuleni ndi kundilanditsa m’madzi ambiri.+Mundilanditse m’manja mwa anthu achilendo,   Anthu amene amalankhula zinthu zonama,+Amenenso dzanja lawo lamanja limachita zachinyengo.+   Inu Mulungu, ine ndidzakuimbirani nyimbo yatsopano.+Ndidzaimba nyimbo yokutamandani ndi choimbira cha zingwe 10. 10  Ndidzaimbira inu amene mumapulumutsa mafumu,Amene mumalanditsa ine Davide mtumiki wanu ku lupanga lovulaza. 11  Ndimasuleni ndi kundilanditsa m’manja mwa anthu achilendo,Anthu amene amalankhula zinthu zonama,Amenenso dzanja lawo lamanja limachita zachinyengo.+ 12  Anthuwo amanena kuti: “Ana athu aamuna, mu unyamata wawo, ali ngati mitengo imene yangokhwima kumene,+Ndipo ana athu aakazi ali ngati mizati yapakona yosemedwa mwaluso ya m’nyumba ya mfumu. 13  Nkhokwe zathu ndi zodzaza ndi zakudya zosiyanasiyana.+Nkhosa zathu zikuswana kukhala masauzandemasauzande. Nkhosa imodzi ikukhala masauzande 10 m’misewu. 14  Ng’ombe zathu zili ndi bere, sizikuvulala kapena kubereka ana akufa,+Ndipo palibe munthu amene akulira m’mabwalo athu.+ 15  Odala ndi anthu amene zimenezi zikuwachitikira.”Ayi, koma odala ndi anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.+

Mawu a M'munsi