Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 143:1-12

Nyimbo ya Davide. 143  Inu Yehova, imvani pemphero langa.+ Tcherani khutu pamene ndikuchonderera.+ Ndiyankheni mogwirizana ndi kukhulupirika kwanu ndi chilungamo chanu.+   Musandiimbe mlandu ine mtumiki wanu,+ Pakuti palibe aliyense wamoyo amene angakhale wolungama pamaso panu.+   Mdani akufunafuna moyo wanga,+ Iye waupondaponda pafumbi.+ Wandichititsa kukhala m’malo a mdima ngati anthu amene anafa kalekale.+   Mtima wanga+ walefuka, Ndipo wachita dzanzi.+   Ndakumbukira masiku akale.+ Ndasinkhasinkha zochita zanu zonse,+ Ndipo ndakhala ndikuganizira ntchito ya manja anu ndi mtima wonse.+   Ine ndikupemphera nditakweza manja anga kwa inu.+ Moyo wanga uli ngati dziko louma limene likulakalaka kuti muthetse ludzu lake.+ [Seʹlah.]   Fulumirani, ndiyankheni inu Yehova.+ Mphamvu zanga zatha.+ Musandibisire nkhope  yanu,+ Chifukwa mukatero ndikhala ngati anthu amene akutsikira kudzenje la manda.+   M’mawa ndichititseni kumva za kukoma mtima kwanu kosatha,+ Pakuti ndimadalira inu.+ Ndidziwitseni njira imene ndiyenera kuyendamo,+ Pakuti ndapereka moyo wanga kwa inu.+   Ndilanditseni kwa adani anga, inu Yehova.+ Ine ndathawira kwa inu.+ 10  Ndiphunzitseni kuchita chifuniro chanu,+ Pakuti inu ndinu Mulungu wanga.+ Mzimu wanu ndi wabwino.+ Unditsogolere m’dziko la olungama.+ 11  Inu Yehova, ndisungenibe wamoyo+ chifukwa cha dzina lanu.+ Chotsani moyo wanga m’masautso+ monga mwa chilungamo chanu.+ 12  Adani anga muwakhalitse chete monga mwa kukoma mtima kwanu kosatha.+ Ndipo muwononge onse ondichitira zoipa,+ Pakuti ine ndine mtumiki wanu.+

Mawu a M'munsi