Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 142:1-7

Masikili.* Salimo ndiponso pemphero la Davide, pamene anali kukhala kuphanga.+ 142  Ndinafuulira Yehova kuti andithandize.+ Ndinafuulira Yehova kuti andikomere mtima.+   Ndinapitirizabe kumukhuthulira nkhawa zanga.+ Ndinapitirizabe kumuuza masautso anga.+   Ndinachita zimenezi pamene mtima wanga+ unalefuka. Pamenepo, munadziwa njira yanga.+ Adani anga anditchera  msampha+ M’njira imene ndikuyenda.+   Yang’anani kudzanja lamanja ndipo muone Kuti palibe aliyense amene akufuna kundithandiza.+ Ndilibenso malo othawirako,+ Ndipo palibe amene akufunsa za moyo wanga.+   Ndinafuula kwa inu kuti mundithandize, inu Yehova.+ Ndinanena kuti: “Inu ndinu pothawirapo panga,+ Gawo langa+ m’dziko la amoyo.”+   Mvetserani kulira kwanga kochonderera,+ Pakuti ndasautsika koopsa.+ Ndipulumutseni kwa anthu amene akundizunza,+ Pakuti iwo ndi amphamvu kuposa ine.+   Nditulutseni mundende ya mdima+ Kuti nditamande dzina lanu.+ Chititsani kuti anthu olungama asonkhane ndi kundizungulira,+ Chifukwa mumandichitira zabwino.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Sl 32:Kamutu.