Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 141:1-10

Nyimbo ya Davide. 141  Inu Yehova, ine ndakuitanani.+ Bwerani kwa ine mofulumira.+ Tcherani khutu pamene ndikukuitanani.+   Pemphero langa likhale lokonzedwa ngati zofukiza+ pamaso panu,+ Mapembedzero anga akhale ngati nsembe yambewu yamadzulo.+   Inu Yehova, ikani mlonda pakamwa panga.+ Ikani wolondera patsogolo pa milomo yanga.+   Musachititse mtima wanga kukonda choipa chilichonse,+ Kuti ndisamachite zinthu zoipa zonditchukitsa,+ Pamodzi ndi amene amachita zinthu zopweteka anzawo,+ Kuti ndisadye chakudya chawo chapamwamba.+   Wolungama akandimenya ndiye kuti wandisonyeza kukoma mtima kosatha,+ Ndipo akandidzudzula ndiye kuti wandidzoza mafuta pamutu panga,+ Mafuta amene mutu wanga sungawakane.+ Pakuti ndidzapemphererabe anthu olungama ngakhale pamene masoka awagwera.+   Oweruza awo awagwetsera pansi m’mphepete mwa thanthwe,+ Koma anthu awo amva zonena zanga ndipo aona kuti ndi zabwino.+   Mafupa athu amwazika pakamwa pa Manda, Mofanana ndi zidutswa zimene zimamwazika pansi pamene munthu akuwaza ndi kung’amba mtengo.+   Koma ine maso anga ali pa inu+ Yehova Ambuye Wamkulu Koposa.+ Ndathawira kwa inu.+ Musalole kuti moyo wanga uwonongeke.+   Nditetezeni kuti ndisagwidwe pamsampha umene anditchera,+ Kuti ndisakodwe ndi makhwekhwe a anthu ochita zopweteka anzawo.+ 10  Oipa onse adzagwera m’maukonde awo omwe,+ Koma ine ndidzadutsa bwinobwino.

Mawu a M'munsi