Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 140:1-13

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide. 140  Inu Yehova, ndilanditseni kwa anthu oipa.+ Nditetezeni kwa munthu wochita zachiwawa,+   Anthu amene amakonza chiwembu mumtima mwawo,+ Amene amandiukira tsiku lonse ngati mmene zimakhalira pankhondo.+   Anola lilime lawo ndipo lakhala ngati la njoka.+ M’milomo yawo muli poizoni wa mphiri.+ [Seʹlah.]   Inu Yehova, ndithandizeni kuti manja a munthu woipa asandikhudze.+ Nditetezeni kwa munthu wochita zachiwawa.+ Nditetezeni kwa anthu amene andikonzera  chiwembu kuti andikankhe ndi kundigwetsa.+   Anthu odzikweza anditchera msampha.+ Iwo aika zingwe ponseponse ngati ukonde m’mphepete mwa njira,+ Ndipo anditchera makhwekhwe.+ [Seʹlah.]   Ndauza Yehova kuti: “Inu ndinu Mulungu wanga.+ Tcherani khutu, inu Yehova, ku mawu anga ochonderera.”+   Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa,+ mpulumutsi wanga wamphamvu,+ Mwatchinga ndi kuteteza mutu wanga pa tsiku lankhondo.+   Inu Yehova, munthu woipa musam’patse zimene mtima wake umafuna.+ Musalole kuti chiwembu chawo chitheke chifukwa angadzikweze.+ [Seʹlah.]   Kunena za anthu amene andizungulira,+ Zoipa zotuluka pakamwa pawo ziphimbe mitu yawo.+ 10  Muwakhuthulire makala oyaka moto pamutu pawo.+ Muwachititse kugwera m’moto+ ndi m’madzi akuya kuti asanyamukenso.+ 11  Munthu wolankhula zazikulu* asakhazikike padziko lapansi.+ Zoipa zisakesake munthu wochita zachiwawa  ndipo zimukanthe mobwerezabwereza.+ 12  Ndikudziwa bwino kwambiri kuti Yehova adzazengera+ Mlandu anthu osautsika. Iye adzachitira chilungamo anthu osauka.+ 13  Ndithudi, anthu olungama adzatamanda dzina lanu.+ Anthu owongoka mtima adzakhalabe pamaso panu.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “woneneza.” Mawu ake enieni ndi “munthu wa lilime.”