Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 14:1-7

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide. 14  Wopusa amanena mumtima mwake kuti: “Kulibe Yehova.”+ Anthu oterewa amachita zoipa,+ ndipo amachita zinthu zonyansa. Palibe amene akuchita zabwino.+   Koma kuchokera kumwamba, Yehova wayang’ana ana a anthu padziko lapansi,+ Kuti aone ngati pali aliyense wozindikira, aliyense amene akufunafuna Yehova.+   Onse apatuka,+ ndipo onsewo ndi achinyengo.+ Palibe aliyense amene akuchita zabwino,+ Palibiretu ndi mmodzi yemwe.+   Kodi palibe aliyense wozindikira mwa anthu ochita zopweteka anzawowa,+ Amene akudya anthu anga ngati chakudya?+ Iwo sanaitane pa Yehova.+   Nthawi yomweyo anagwidwa ndi mantha aakulu,+ Pakuti Yehova ali pakati pa khamu* la anthu olungama.+   Anthu inu mumanyazitsa malangizo a munthu wosautsika, Chifukwa Yehova ndiye pothawirapo pake.+   Haa! Zikanakhala bwino m’Ziyoni mukanapezeka chipulumutso cha Isiraeli.+ Yehova akadzasonkhanitsa ndi kubwezeretsa anthu ake amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,+ Yakobo adzasangalale, Isiraeli adzakondwere.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “m’badwo.”