Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 139:1-24

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la Davide. 139  Inu Yehova, mwandifufuza ndipo mukundidziwa.+   Inu mumadziwa ndikakhala pansi kapena ndikaimirira.+ Mumadziwa maganizo anga muli kutali.+   Mumandidziwa bwino pamene ndikuyenda komanso pamene ndikugona,+ Ndipo njira zanga zonse mukuzidziwa bwino.+   Ndisananene kanthu,+ Inu Yehova mumakhala mutadziwa kale zonse.+   Mwandizungulira, Ndipo mwaika dzanja lanu pa ine.   Kwa ine ndi zovuta kwambiri kuti ndidziwe zinthu zonsezi.+ Ndi zapamwamba kwambiri moti sindingathe kuzifikira.+   Ndingapite kuti kuthawa mzimu wanu,+ Ndipo ndingapite kuti kuthawa nkhope yanu?+   Ngati ndingakwere kumwamba, inu mudzakhala komweko.+ Ndipo ngati ndingayale bedi langa ku Manda, taonani! inunso mudzakhala komweko.+   Ngati ndingakwere pamapiko+ a m’bandakucha, Kuti ndikakhale m’nyanja ya kutali kwambiri,+ 10  Kumenekonso dzanja lanu lidzanditsogolera,+ Dzanja lanu lamanja lidzandigwira.+ 11  Ngati ndinganene kuti: “Ndithudi mdima undipeze mofulumira!”+ Pamenepo mdima udzasanduka kuwala pa ine.+ 12  Ndipo mdimawo sudzakhala mdima wandiweyani kwa inu,+ Koma usiku udzakuwalirani ngati masana.+ Mdima udzangokhala ngati kuwala.+ 13  Inu munapanga impso zanga,+ Ndipo munali kunditchinga m’mimba mwa mayi anga.+ 14  Ndidzakutamandani chifukwa munandipanga modabwitsa ndipo zimenezi zimandichititsa mantha.+ Ntchito zanu ndi zodabwitsa,+ Ndipo ine ndimadziwa bwino zimenezi.+ 15  Mafupa anga sanali obisika kwa inu+ Pamene munali kundipanga m’malo obisika,+ Pamene munali kundiwomba ngati nsalu m’malo apansi kwambiri+ padziko lapansi. 16  Maso anu anandiona pamene ndinali mluza,+ Ndipo ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku lanu. M’bukumo munalembamo za masiku amene zinapangidwa+ Koma panalibe ngakhale chiwalo chimodzi chimene chinali chitapangidwa. 17  Choncho kwa ine maganizo anu ndi ofunika kwambiri,+ inu Mulungu, Ndipo ndi ochuluka zedi.+ 18  Nditati ndiyese kuwawerenga, angakhale ochuluka kwambiri kuposa mchenga.+ Podzuka ndingakhale ndikuwawerengabe.+ 19  Inu Mulungu, zikanakhala bwino mukanapha woipa.+ Pamenepo anthu amene ali ndi mlandu wa magazi+ akanandichokera, 20  Anthu amene amanena zam’mutu mwawo zotsutsana ndi inu.+ Adani anuwo+ agwiritsa ntchito dzina lanu mosasamala.+ 21  Inu Yehova, pajatu ine ndimadana ndi anthu amene amadana nanu kwambiri,+ Ndipo anthu okupandukirani ndimanyansidwa nawo.+ 22  Ndimadana nawo kwambiri.+ Kwa ine akhala adani enieni.+ 23  Ndifufuzeni, inu Mulungu, ndi kudziwa mtima wanga.+ Ndisanthuleni ndi kudziwa malingaliro anga amene akundisowetsa mtendere,+ 24  Ndipo muone ngati mwa ine muli chilichonse chimene chikundichititsa kuyenda m’njira yoipa,+ Ndipo munditsogolere m’njira+ yamuyaya.

Mawu a M'munsi