Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 138:1-8

Salimo la Davide. 138  Ndidzakutamandani ndi mtima wanga wonse.+ Ndidzakuimbirani nyimbo zokutamandani pamaso pa milungu ina.+   Ndidzawerama nditayang’ana kukachisi wanu woyera,+ Ndipo ndidzatamanda dzina lanu+ Chifukwa cha kukoma mtima kwanu kosatha+ ndi choonadi chanu.+ Pakuti malonjezo+ amene munawachita m’dzina lanu ndi aakulu ndithu. Koma kukwaniritsidwa kwa malonjezowo n’kwakukulu koposa.+   Pa tsiku limene ine ndinaitana, inu munandiyankha.+ Munandilimbitsa mtima ndi kundipatsa mphamvu.+   Mafumu onse a padziko lapansi adzakutamandani, inu Yehova,+ Pakuti adzakhala atamva mawu a pakamwa panu.   Ndipo iwo adzaimba za njira za Yehova,+ Pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukulu.+   Ngakhale kuti Yehova ali pamwamba, amaona wodzichepetsa,+ Koma wodzikuza samuyandikira.+   Ndikakhala pa masautso, inu mudzandisunga wamoyo.+ Mudzatambasula dzanja lanu chifukwa cha mkwiyo wa adani anga,+ Ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.+   Yehova adzakwaniritsa zolinga zimene ali nazo pa ine.+ Inu Yehova, kukoma mtima kwanu kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ Musasiye ntchito ya manja anu.+

Mawu a M'munsi