Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 137:1-9

137  Tinakhala pansi+  m’mphepete mwa mitsinje ya ku Babulo,+ Ndipo tinalira titakumbukira Ziyoni.+   Tinapachika azeze athu+ Pamitengo ya msondodzi.+   Kumeneko, amene anatigwira ukapolo anatiuza kuti tiwaimbire nyimbo,+ Ndipo otinyozawo anatipempha kuti tiwasangalatse.+ Iwo anati: “Tiimbireni imodzi mwa nyimbo za ku Ziyoni.”+   Tingaimbe bwanji nyimbo ya Yehova+ M’dziko lachilendo?+   Ndikakuiwala iwe Yerusalemu,+ Dzanja langa lamanja liiwale luso lake.   Lilime langa limamatire m’kamwa mwanga+ Ngati sindingakukumbukire,+ Ngati sindingakweze iwe Yerusalemu Pamwamba pa chilichonse chimene chimandikondweretsa.+   Inu Yehova, kumbukirani+ zimene ana a Edomu+ ananena pa tsiku limene Yerusalemu anawonongedwa,+ Iwo anati: “Fafanizani mzindawo! Ufafanizeni mpaka pamaziko ake!”+   Iwe mwana wamkazi wa Babulo, amene udzafunkhidwa,+ Wodala ndi amene adzakubwezera+ Zimene iwe watichitira.+   Wodala ndi iye amene adzagwira ana ako ndi kuwaphwanya zidutswazidutswa+ Mwa kuwawombetsa pathanthwe.

Mawu a M'munsi