Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Masalimo 136:1-26

136  Yamikani Yehova  anthu inu, pakuti iye ndi wabwino:+ Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+   Yamikani Mulungu wa milungu:+ Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+   Yamikani Mbuye wa ambuye:+ Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+   Yamikani Wochita zodabwitsa ndiponso ntchito zazikulu:+ Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+   Yamikani amene anapanga kumwamba mwanzeru:+ Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+   Yamikani woyala dziko lapansi pamwamba pa madzi:+ Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+   Yamikani wopanga zounikira zazikulu:+ Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+   Amenenso anapanga dzuwa kuti lizilamulira masana:+ Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+   Amene anapanga mwezi ndi nyenyezi kuti zizilamulira pamodzi usiku:+ Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 10  Yamikani amene anakantha Aiguputo mwa kupha ana awo oyamba kubadwa:+ Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 11  Yamikani amene anatulutsa Aisiraeli pakati pawo:+ Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 12  Anawatulutsa ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasula:+ Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale. 13  Yamikani amene anagawa pakati Nyanja Yofiira:+ Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 14  Amenenso anachititsa Isiraeli kudutsa pakati pake:+ Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 15  Amenenso anakutumulira Farao ndi gulu lake lankhondo m’Nyanja Yofiira:+ Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 16  Yamikani amene anayendetsa anthu ake m’chipululu:+ Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 17  Yamikani amene anapha mafumu amphamvu:+ Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 18  Amenenso anapha mafumu olemekezeka:+ Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 19  Iye anapha Sihoni mfumu ya Aamori:+ Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 20  Anaphanso Ogi mfumu ya Basana:+ Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 21  Ndipo dziko lawo analipereka kwa anthu ake kukhala cholowa:+ Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 22  Cholowa cha Isiraeli mtumiki wake:+ Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 23  Iye amene anatikumbukira pamene adani anatinyazitsa:+ Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 24  Amene anatipulumutsa mobwerezabwereza kuchokera m’manja mwa adani athu:+ Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 25  Amenenso amapereka chakudya kwa zamoyo zonse:+ Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 26  Yamikani Mulungu wakumwamba:+ Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

Mawu a M'munsi