Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Masalimo 135:1-21

135  Tamandani Ya, anthu inu!+ Tamandani dzina la Yehova,+ Mutamandeni, inu atumiki a Yehova,+   Inu amene mukuimirira m’nyumba ya Yehova,+ M’mabwalo a nyumba ya Mulungu wathu.+   Tamandani Ya, pakuti Yehova ndi wabwino.+ Muimbireni nyimbo zotamanda dzina lake, pakuti kuchita zimenezi n’kosangalatsa.+   Ya wadzisankhira Yakobo,+ Wadzisankhira Isiraeli kukhala chuma chake chapadera.+   Ine ndikudziwa bwino kuti Yehova ndi wamkulu,+ Ndipo Ambuye wathu ndi woposa milungu ina yonse.+   Chilichonse chimene Yehova anafuna kuchita anachita.+ Anachita zimenezi kumwamba, padziko lapansi, m’nyanja ndi m’madzi onse akuya.+   Amachititsa nthunzi kukwera kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+ Iye anapanganso zipata zotulukirapo mvula.+ Amachititsa mphepo kutuluka m’nkhokwe zake.+   Wochita zimenezi ndiye anapha ana oyamba kubadwa a ku Iguputo,+ Anapha ana a anthu ngakhalenso ana a nyama.+   Anasonyeza zizindikiro ndi kuchita zozizwitsa pakati pako Iguputo iwe,+ Anachita zimenezo kwa Farao ndi kwa atumiki ake onse.+ 10  Amene anachita zimenezi ndi amene anakantha mitundu yambiri+ Ndi kupha mafumu amphamvu.+ 11  Anaphanso Sihoni mfumu ya Aamori+ Ndi Ogi mfumu ya Basana,+ Ndipo anafafaniza maufumu onse a ku Kanani.+ 12  Dziko lawo analipereka kukhala cholowa,+ Cholowa cha anthu ake Aisiraeli.+ 13  Inu Yehova, dzina lanu lidzakhalapo mpaka kalekale.+ Inu Yehova, dzina lanu* lidzakhalapo ku mibadwomibadwo.+ 14  Pakuti Yehova adzaweruzira anthu ake mlandu,+ Ndipo adzamvera chisoni atumiki ake.+ 15  Mafano a anthu a mitundu ina ndi opangidwa ndi siliva ndi golide,+ Ntchito ya manja a munthu wochokera kufumbi.+ 16  Pakamwa ali napo koma salankhula.+ Maso ali nawo koma saona.+ 17  Makutu ali nawo koma satha kumva.+ Komanso m’mphuno mwawo mulibe mpweya.+ 18  Amene amawapanga adzafanana nawo,+ Onse amene amawakhulupirira adzakhala ngati mafanowo.+ 19  Inu nyumba ya Isiraeli, tamandani Yehova.+ Inu nyumba ya Aroni, tamandani Yehova.+ 20  Inu nyumba ya Levi, tamandani Yehova.+ Inu oopa Yehova, tamandani Yehova.+ 21  Yehova amene akukhala ku Yerusalemu,+ Atamandidwe mu Ziyoni.+ Tamandani Ya, anthu inu!+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “chikumbutso chanu.”