Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 132:1-18

Nyimbo Yokwerera Kumzinda. 132  Inu Yehova, kumbukirani Davide,+ Kumbukirani masautso ake onse.+   Kumbukirani kuti analumbira kwa inu Yehova,+ Analonjeza kwa Wamphamvu+ wa Yakobo kuti:+   “Sindilowa m’nyumba yanga.+ Sindigona pabedi langa.+   Maso anga saona tulo,+ Ndipo sindilola maso anga owala kuwodzera,+   Kufikira Yehova nditamupezera nyumba,+ Kufikira nditapeza chihema chachikulu cha Wamphamvu wa Yakobo.”+   Taonani! Tamva za Likasa* ku Efurata,+ Talipeza kunkhalango.+   Tiyeni tilowe m’chihema chake chachikulu.+ Tiyeni tiwerame pachopondapo mapazi ake.+   Nyamukani, inu Yehova, kuti mulowe kumalo anu okhalamo,+ Inu pamodzi ndi Likasa+ limene mumasonyezera mphamvu zanu.+   Ansembe anu avale chilungamo,+ Ndipo okhulupirika anu afuule mosangalala.+ 10  Chifukwa cha zimene munalonjeza Davide mtumiki wanu,+ Musakane kuona nkhope ya wodzozedwa wanu.+ 11  Yehova walumbira kwa Davide,+ Ndithudi sadzabweza mawu ake akuti:+ “Ndidzaika pampando wako wachifumu+ Chipatso cha mimba yako.+ 12  Ana ako akadzasunga pangano langa+ Ndi zikumbutso zanga zimene ndidzawapatsa,+ Ngakhalenso ana awo+ Adzakhala pampando wako wachifumu kwamuyaya.”+ 13  Yehova wasankha Ziyoni,+ Ndipo amafunitsitsa kuti akhale malo ake okhalamo. Iye amati:+ 14  “Awa ndi malo anga okhalamo mpaka muyaya.+ Ndidzakhala mmenemu, pakuti ndimafunitsitsa kukhala m’malo amenewa.+ 15  Ndithu ndidzadalitsa chakudya chake.+ Anthu ake osauka ndidzawapatsa chakudya chokwanira.+ 16  Ansembe ake ndidzawaveka chipulumutso,+ Ndipo anthu ake okhulupirika adzafuula ndithu mokondwera. 17  Ku Ziyoniko ndidzakulitsa nyanga* ya Davide.+ Wodzozedwa wanga ndamukonzera nyale.+ 18  Adani ake ndidzawaveka manyazi,+ Koma ufumu*+ wake udzapita patsogolo.”+

Mawu a M'munsi

Kapena “Chihema.”
Onani mawu a m’munsi pa 1Sa 2:1.
Mawu ake enieni, “chisoti chachifumu.”