Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 130:1-8

Nyimbo Yokwerera Kumzinda. 130  Inu Yehova, pa nthawi imene zinthu zinandivuta kwambiri ndinaitana pa inu.+   Imvani mawu anga Yehova.+ Makutu anu amve mawu anga ochonderera.+   Inu Ya, mukanakhala kuti mumayang’anitsitsa  zolakwa,+ Ndani akanaima pamaso panu, inu Yehova?+   Inu mumakhululukiradi,+ Kuti anthu akuopeni.+   Ndayembekezera thandizo lanu, inu Yehova. Moyo wanga wayembekezera thandizo lanu.+ Ine ndayembekezera mawu anu.+   Ndayembekezera Yehova+ Kuposa alonda amene akuyembekezera kuti kuche,+ Ndithu kuposa alonda amene akuyembekezera kuti kuche.+   Isiraeli ayembekezere Yehova,+ Pakuti Yehova amasonyeza kukoma mtima kosatha.+ Iye ali ndi mphamvu zochuluka zowombolera anthu ake.+   Iye adzawombola Isiraeli ku zolakwa zake zonse.+

Mawu a M'munsi