Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 13:1-6

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide. 13  Kodi mudzandiiwala kufikira liti, inu Yehova?+ Mpaka muyaya?+ Mudzandibisira nkhope yanu kufikira liti?+   Kodi ndidzalimbana ndi masautso anga kufikira liti? Kodi masiku a moyo wanga adzakhala odzaza ndi chisoni kufikira liti? Kodi mdani wanga adzadzikweza pamaso panga kufikira liti?+   Ndiyang’aneni. Ndiyankheni, inu Yehova Mulungu wanga. Walitsani maso anga+ kuti ndisagone mu imfa.+   Chitani zimenezi kuti mdani wanga asanene kuti: “Ndamugonjetsa!” Kutinso adani anga asakondwere chifukwa chakuti ine ndadzandira.+   Koma ine ndakhulupirira kukoma mtima kwanu kosatha.+ Mtima wanga ukondwere chifukwa cha chipulumutso chanu.+   Ndidzaimbira Yehova chifukwa wandifupa ndi zinthu zabwino.+

Mawu a M'munsi