Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 129:1-8

Nyimbo Yokwerera Kumzinda. 129  “Andisonyeza chidani mokwanira kuyambira ndili mnyamata,”+Isiraeli anene kuti,+   “Andisonyeza chidani mokwanira kuyambira ndili mnyamata,+Koma sanandigonjetse.+   Olima ndi ng’ombe andilima pamsana.*+Iwo alima mizere italiitali.”   Yehova ndi wolungama.+Iye waduladula zingwe za oipa.+   Onse odana ndi Ziyoni,+Adzachita manyazi ndipo adzatembenuka ndi kubwerera okha.+   Adzakhala ngati udzu wanthete womera padenga,+Umene umauma asanauzule,+   Umene wokolola sanadzaze nawo manja ake,+Ngakhalenso aliyense amene akunyamula mitolo ya zokolola sanadzaze nawo thumba lake la pachifuwa.   Anthu odutsa nawonso sananene kuti:“Madalitso a Yehova akhale nanu anthu inu.+Takudalitsani m’dzina la Yehova.”+

Mawu a M'munsi

Zikuoneka kuti apa akunena za nkhanza zimene mitundu ina yodana nawo inawachitira.