Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 128:1-6

Nyimbo Yokwerera Kumzinda. 128  Wodala ndi aliyense woopa Yehova,+ Amene amayenda m’njira za Mulungu.+   Pakuti udzadya zipatso za ntchito ya manja ako.+ Udzakhala wodala ndipo zinthu zidzakuyendera bwino.+   Mkazi wako adzakhala ngati mtengo wa mpesa wobala zipatso+ Mkati mwa nyumba yako. Ana ako adzakhala ngati mphukira za mitengo ya maolivi+ kuzungulira tebulo lako.   Taonani! Mwamuna aliyense wamphamvu woopa Yehova+ Adzadalitsidwa mwa njira imeneyi.+   Yehova adzakudalitsa ali ku Ziyoni.+ Komanso usangalale ndi zinthu zabwino za mu Yerusalemu masiku onse a moyo wako,+   Ndipo uone ana a ana ako.+ Mtendere ukhale pa Isiraeli.+

Mawu a M'munsi