Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 127:1-5

Nyimbo ya Solomo Yokwerera Kumzinda. 127  Yehova akapanda kumanga nyumba,Omanga nyumbayo amagwira ntchito pachabe.+Yehova akapanda kulondera mzinda,Alonda amakhala maso pachabe.+   Anthu inu mukudzuka m’mawa pachabe,+Mukungovutika kugwira ntchito mpaka usiku,Mukudya chakudya chimene mwachipeza movutikira.Koma Mulungu amapereka tulo kwa wokondedwa wake.+   Taonani! Ana ndi cholowa chochokera kwa Yehova.Chipatso cha mimba ndicho mphoto.   Ana a bambo wachinyamata+Ali ngati mivi m’dzanja la mwamuna wamphamvu.+   Wodala ndi mwamuna wamphamvu amene wadzaza kachikwama kake ka mivi ndi mivi imeneyo.Abambo oterowo sadzachita manyazi,+Pakuti anawo adzalankhula ndi adani pachipata.

Mawu a M'munsi