Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 126:1-6

Nyimbo Yokwerera Kumzinda. 126  Pamene Yehova anasonkhanitsa ndi kubwezeretsa ogwidwa ukapolo a Ziyoni,+ Tinakhala ngati tikulota.+   Pa nthawiyo tinaseka kwambiri,+ Ndipo lilime lathu linatulutsa mawu okondwa.+ Pamenepo anthu a mitundu ina anayamba kuuzana kuti:+ “Yehova wachitira anthu amenewa zinthu zazikulu.”+   Yehova watichitira zazikulu.+ Tasangalala.+   Sonkhanitsani ndi kubwezeretsa gulu lathu logwidwa ukapolo inu Yehova,+ Ngati mmene mumabwezeretsera madzi m’mitsinje ya ku Negebu.+   Amene akukhetsa misozi pofesa mbewu,+ Adzakolola akufuula mosangalala.+   Amene akupita kumunda akulira,+ Atasenza thumba lodzaza mbewu,+ Adzabwerako akufuula mosangalala,+ Atasenza mtolo wake wa zokolola.+

Mawu a M'munsi