Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 125:1-5

Nyimbo Yokwerera Kumzinda. 125  Okhulupirira Yehova+ Ali ngati phiri la Ziyoni,+ limene silingagwedezeke,  koma lidzakhalapo mpaka kalekale.+   Yehova wazungulira anthu ake+ Ngati mmene mapiri azungulirira Yerusalemu,+ Kuyambira tsopano mpaka kalekale.+   Ndodo yachifumu ya oipa sidzapitiriza kukhala+ padziko limene olungama analandira monga cholowa chawo, Kuti olungamawo asatambasule dzanja lawo ndi kuchita choipa.+   Inu Yehova, chitirani zabwino anthu abwino,+ Anthu owongoka mtima.+   Koma anthu obwerera kunjira zawo zokhotakhota,+ Yehova adzawapereka ku chilango pamodzi ndi ochita zopweteka anzawo.+ Ndipo mu Isiraeli mudzakhala mtendere.+

Mawu a M'munsi