Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 124:1-8

Nyimbo ya Davide Yokwerera Kumzinda. 124  “Yehova akanapanda kukhala kumbali yathu,”+ Isiraeli anene kuti,+   “Yehova akanapanda kukhala kumbali yathu,+ Pamene anthu anatiukira,+   Akanatimeza amoyo,+ Pamene mkwiyo wawo unatiyakira.+   Pamenepo madzi akanatikokolola,+ Mtsinje wamphamvu ukanatimiza.+   Madzi amphamvu Akanatimiza.+   Yehova atamandike, chifukwa sanatipereke kwa iwo+ Kuti atikhadzule ngati nyama.+   Moyo wathu uli ngati mbalame imene yathawa+ Pamsampha wa munthu wogwiritsa ntchito nyambo.+ Msamphawo wathyoka,+ Ndipo ife tapulumuka.+   Thandizo lathu lili m’dzina la Yehova,+ Wopanga kumwamba ndi dziko lapansi.”+

Mawu a M'munsi