Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 123:1-4

Nyimbo Yokwerera Kumzinda. 123  Ndakweza maso anga kuyang’ana inu,+ Kuyang’ana inu amene mukukhala kumwamba.+   Taonani! Monga mmene maso a atumiki amayang’anira dzanja la mbuye wawo,+ Mmene maso a kapolo wamkazi amayang’anira dzanja la mbuye wake wamkazi,+ Momwemonso, maso athu adzayang’ana kwa Yehova Mulungu wathu,+ Kufikira atatikomera mtima.+   Tikomereni mtima, inu Yehova, tikomereni mtima,+ Pakuti tanyozeka kwambiri.+   Moyo wathu wasautsika kwambiri chifukwa cha kunyoza kwa anthu amene akukhala mosatekeseka,+ Ndiponso chifukwa cha kunyoza kwa anthu odzikuza.+

Mawu a M'munsi