Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 122:1-9

Nyimbo ya Davide Yokwerera Kumzinda. 122  Ndinakondwera pamene anandiuza kuti:+ “Tiyeni tipite+ kunyumba ya Yehova.”+   Mapazi athu anaima+ Pazipata zako iwe Yerusalemu.+   Mzinda wa Yerusalemu unamangidwa+ Ngati chinthu chimodzi chogwirizana,+   Mafuko amapita kumeneko,+ Mafuko a Ya,+ Amapita kumeneko kukatamanda dzina la Yehova+ Mogwirizana ndi lamulo loperekedwa kwa Isiraeli.+   Kumeneko n’kumene kumakhala mipando yachiweruzo,+ Mipando yachifumu ya nyumba ya Davide.+   Pemphererani mtendere wa Yerusalemu, anthu inu.+ Amene amakukonda, mzinda iwe, sadzakhala ndi nkhawa iliyonse.+   M’malo ako otchingidwa ndi khoma lolimba mupitirizebe kukhala mtendere,+ Anthu okhala munsanja zako apitirizebe kukhala opanda nkhawa iliyonse.+   Tsopano ndikulankhula m’malo mwa abale anga ndi anzanga kuti:+ “Mtendere ukhale nawe.”+   Chifukwa cha nyumba ya Yehova Mulungu wathu,+ Ndidzapitiriza kukupempherera kuti zinthu zikuyendere bwino.+

Mawu a M'munsi