Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 121:1-8

Nyimbo Yokwerera Kumzinda. 121  Ndakweza maso anga kuyang’ana kumapiri.+Kodi thandizo langa lichokera kuti?+   Thandizo langa lichokera kwa Yehova,Wopanga kumwamba ndi dziko lapansi.+   Iye sangalole kuti phazi lako lipunthwe.Amene amakuyang’anira sangawodzere.+   Taonani! Amene akuyang’anira Isiraeli,+Sangawodzere kapena kugona.+   Yehova akukuyang’anira.Yehova ndiye mthunzi wako+ kudzanja lako lamanja.+   Masana dzuwa silidzakupweteka,+Kapenanso mwezi usiku.+   Yehova adzakuteteza ku masoka onse.+Iye adzateteza moyo wako.+   Yehova adzakuteteza pa zochita zako zonse,Kuyambira tsopano mpaka kalekale.+

Mawu a M'munsi