Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 120:1-7

Nyimbo Yokwerera Kumzinda. 120  Ndinafuulira Yehova m’masautso anga,+ Ndipo iye anandiyankha.+   Inu Yehova, ndilanditseni ku milomo yonama,+ Ndi ku lilime lachinyengo.+   Kodi iwe lilime lachinyengo,+ Munthu adzakupatsa chiyani ndipo adzawonjezera chiyani pa iwe?   Adzakupatsa mivi yakuthwa ya munthu wamphamvu,+ Pamodzi ndi makala amoto a mtengo wa m’chipululu.+   Tsoka kwa ine! Chifukwa ndakhala mlendo m’dziko la Meseke.+ Ndakhala muhema pakati pa mahema a Kedara.+   Ndakhala mumsasa nthawi yaitali+ Pamodzi ndi anthu odana ndi mtendere.+   Ndimalimbikitsa mtendere,+ koma ndikalankhula, Iwo amafuna nkhondo.+

Mawu a M'munsi