Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 12:1-8

Kwa wotsogolera nyimbo: Iimbidwe chapansipansi.*+ Nyimbo ya Davide. 12  Ndipulumutseni,+ inu Yehova, pakuti anthu okhulupirika atha.+ Anthu okhulupirika atheratu pakati pa ana a anthu.   Iwo amalankhulana zabodza.+ Amalankhulana ndi milomo yoshashalika+ komanso ndi mitima iwiri.+   Yehova adzadula milomo yonse yolankhula zachinyengo Ndi lilime lolankhula modzikuza.+   Iye adzadula anthu onena kuti: “Ndi lilime lathu tidzapambana.+ Timalankhula chilichonse chimene tikufuna ndi milomo yathu. Ndani angatilamulire?”   Tsopano Yehova wanena kuti: “Chifukwa cha kuponderezedwa kwa osautsika, chifukwa cha kuusa moyo kwa anthu osauka,+ Ndidzanyamuka pa nthawiyo,+ Ndidzawateteza kwa aliyense wowanyodola.”+   Mawu a Yehova ndi oyengeka bwino,+ Ngati siliva woyengedwa nthawi zokwanira 7 mung’anjo ya m’nthaka.   Inu Yehova mudzawayang’anira.+ Aliyense wa iwo mudzamuteteza ku m’badwo uwu mpaka kalekale.   Anthu oipa akuyendayenda ponseponse, Chifukwa ana a anthu amayamikira zoipa.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Sl 6:Kamutu.