Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 119:1-176

א [ʼAʹleph] 119  Odala ndi anthu osalakwitsa kanthu m’njira zawo,Anthu amene akutsatira chilamulo cha Yehova.+   Odala ndi anthu amene amasunga zikumbutso zake,+Amene amayesetsa kumufunafuna ndi mtima wonse.   Ndithu, iwo sachita chinthu chosalungama.Amayenda m’njira zake.   Inu mwatilamula kuti tisungeMalamulo anu mosamala.+   Haa! Ndikanakonda kuti ndiyende mowongoka+Kuti ndisunge malangizo anu,   Pamenepo sindikanachita manyazi,+Pamene ndikulabadira malamulo anu onse.   Ndidzakutamandani ndi mtima wowongoka,Pamene ndikuphunzira zigamulo zanu zolungama.   Ndikupitiriza kusunga malangizo anu,Choncho musandisiyiretu.+ ב [Behth]   Kodi wachinyamata+ angakhale bwanji woyera pa moyo wake?Mwa kudziyang’anira ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi mawu anu.+  10  Ndayesetsa kukufunafunani ndi mtima wanga wonse.Musandichititse kusochera ndi kuchoka pa malamulo anu.+  11  Ndasunga mosamala mawu anu mumtima mwanga,+Kuti ndisakuchimwireni.+  12  Ndinu wodala inu Yehova.Ndiphunzitseni malamulo anu.  13  Ndi milomo yanga ndalengeza+Zigamulo zonse zotuluka pakamwa panu.  14  Ndimakondwera kuyenda m’njira ya zikumbutso zanu,+Ngati mmene anthu amachitira akapeza chuma chilichonse chamtengo wapatali.+  15  Ndidzasinkhasinkha malamulo anu,+Ndipo ndidzalabadira njira zanu.+  16  Ndidzakonda malamulo anu.Ndipo sindidzaiwala mawu anu. ג [Giʹmel]  17  Ndichitireni zabwino, ine mtumiki wanu, kuti ndikhale ndi moyo,Ndi kuti ndisunge mawu anu.+  18  Tsegulani maso anga kuti ndione+Zinthu zodabwitsa za m’chilamulo chanu.+  19  Ine ndine mlendo m’dziko ili.Musandibisire malamulo anu.  20  Moyo wanga wasautsika chifukwa cholakalaka+Zigamulo zanu nthawi zonse.  21  Mwadzudzula odzikuza otembereredwa,+Amene akusochera ndi kuchoka pa malamulo anu.+  22  Mugubuduze ndi kuchotsa chitonzo ndi kunyozedwa kwanga,Pakuti ndasunga zikumbutso zanu.+  23  Akalonga asonkhana pamodzi kuti akambirane zondiukira.+Koma ine mtumiki wanu, ndimasinkhasinkha malangizo anu.  24  Ndimakonda zikumbutso zanu,+Ndipo zili ngati anthu amene amandipatsa malangizo. ד [Daʹleth]  25  Moyo wanga wamamatira kufumbi.+Ndisungeni wamoyo mogwirizana ndi mawu anu.  26  Ndakuuzani za njira zanga kuti mundiyankhe.Ndiphunzitseni malamulo anu.  27  Ndithandizeni kumvetsa njira zofotokozedwa m’malamulo anu,+Kuti ndisinkhesinkhe ntchito zanu zodabwitsa.  28  Ine ndikusowa tulo chifukwa cha chisoni.+Ndilimbitseni ndi mawu anu.+  29  Ndichotsereni njira yolakwika,+Ndikomereni mtima mwa kundipatsa chilamulo chanu.+  30  Ine ndasankha kuyenda mokhulupirika.+Zigamulo zanu ndimaziona kukhala zoyenera.  31  Ndamamatira zikumbutso zanu.+Inu Yehova, musandichititse manyazi.+  32  Ndidzamvera malamulo anu,Chifukwa mwandichititsa kuwamvetsa bwino. ה [Heʼ]  33  Ndilangizeni inu Yehova, kuti ndiyende motsatira malangizo anu,+Kuti nditsatire malangizo anu moyo wanga wonse.+  34  Ndithandizeni kukhala wozindikira kuti nditsatire chilamulo chanu,+Ndiponso kuti ndichisunge ndi mtima wonse.+  35  Ndiyendetseni m’njira ya malamulo anu,+Pakuti ndikukondwera ndi njira imeneyi.+  36  Ndithandizeni kuti mtima wanga uziganizira zikumbutso zanu,+Osati kupeza phindu.*  37  Chititsani maso anga kuti asaone zinthu zopanda pake.Ndiyendetseni m’njira yanu kuti ndikhalebe wamoyo.+  38  Kwaniritsani mawu anu pa mtumiki wanu,Mawu amene amachititsa mtumiki wanu kukuopani.+  39  Ndichotsereni chitonzo chimene ndikuchiopa,+Pakuti zigamulo zanu ndi zabwino.  40  Taonani! Ine ndikulakalaka malamulo anu.+Ndisungeni wamoyo mogwirizana ndi chilungamo chanu.+ ו [Waw]  41  Monga mwa mawu anu, inu Yehova, ndipatseni chipulumutso chanu.Ndipatseni zochita zanu zosonyeza kukoma mtima kosatha,+  42  Kuti ndipeze choyankha kwa wonditonza,+Pakuti ine ndakhulupirira mawu anu.+  43  Musachotse mawu a choonadi pakamwa panga,+Pakuti ndayembekezera chigamulo chanu.  44  Ndidzasunga chilamulo chanu nthawi zonse,+Mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+  45  Ndidzayenda uku ndi uku m’malo otakasuka,+Chifukwa ndaphunzira malamulo anu ndi kuwasunga.+  46  Komanso ndidzanena za zikumbutso zanu pamaso pa mafumu,Ndipo sindidzachita manyazi.+  47  Ndidzakondwera ndi malamulo anu+Amene ndimawakonda.+  48  Ndidzapemphera kwa inu nditakweza manja anga chifukwa ndimakonda malamulo anu,+Ndipo ndidzasinkhasinkha malangizo anu.+ ז [Zaʹyin]  49  Kumbukirani mawu amene munandiuza ine mtumiki wanu,Mawu amene ndikuwayembekezera malinga ndi lonjezo lanu.+  50  Chimenechi ndi chilimbikitso changa mu nsautso yanga,+Pakuti mawu anu andisungabe wamoyo.+  51  Anthu odzikuza andinyoza koopsa.+Koma ine sindinapatuke pa chilamulo chanu.+  52  Ndimakumbukira zigamulo zanu zakalekale inu Yehova,Ndipo zimandilimbikitsa.+  53  Mkwiyo ukuyaka mumtima mwanga chifukwa cha oipa,Amene akusiya chilamulo chanu.+  54  Kwa ine, malangizo anu akhala ngati nyimbo zokutamandani,+M’nyumba zimene ndimakhala m’mayiko achilendo.  55  Usiku ndimakumbukira dzina lanu, inu Yehova,+Kuti ndisunge chilamulo chanu.+  56  Ndi zimenetu zandichitikira ine,Chifukwa ndimatsatira malamulo anu.+ ח [Chehth]  57  Yehova, inu ndiye cholowa changa.+Ndalonjeza kusunga mawu anu.  58  Ndayesetsa ndi mtima wanga wonse kuti mundiyanje.*Ndikomereni mtima monga mwa mawu anu.+  59  Ndaganizira mozama za njira zanga,+Kuti mapazi anga ndiwabwezere ku zikumbutso zanu.  60  Ndinafulumira ndipo sindinazengerezeKusunga malamulo anu.+  61  Zingwe za oipa zinandikulunga,+Koma ine sindinaiwale chilamulo chanu.  62  Pakati pa usiku ndimadzuka kuti ndikuyamikeni+Chifukwa cha zigamulo zanu zolungama.  63  Ine ndine mnzawo wa anthu okuopani,+Ndiponso wa anthu osunga malamulo anu.+  64  Inu Yehova, kukoma mtima kwanu kosatha kwadzaza dziko lonse lapansi.+Ndiphunzitseni malamulo anu. ט [Tehth]  65  Inu Yehova, mwandichitiradi zabwino ine mtumiki wanu,Monga mwa mawu anu.+  66  Ndiphunzitseni kuchita zabwino,+ kulingalira bwino ndi kudziwa zinthu,Pakuti ndimakhulupirira malamulo anu.+  67  Ndisanagwe m’masautso ndinali kuchimwa mosadziwa,Koma tsopano ndimasunga mawu anu.+  68  Inu ndinu wabwino ndipo mukuchita zabwino.+Ndiphunzitseni malamulo anu.+  69  Anthu odzikuza andinenera mabodza ambiri,+Koma ine ndidzasunga malamulo anu ndi mtima wanga wonse.+  70  Mitima yawo yauma ngati mafuta oundana,+Koma ine ndimakonda chilamulo chanu.+  71  Zili bwino kuti ndasautsika,+Kuti ndiphunzire malamulo anu.  72  Chilamulo chotuluka pakamwa panu n’chabwino kwa ine,+N’chabwino kwambiri kuposa ndalama masauzande zagolide ndi zasiliva.+ י [Yohdh]  73  Manja anu anandipanga, ndipo anandiumba.+Ndithandizeni kukhala wozindikira, kuti ndiphunzire malamulo anu.  74  Oopa inu ndi amene amasangalala akandiona,+Chifukwa ndayembekezera mawu anu.+  75  Inu Yehova, ndikudziwa bwino kuti zigamulo zanu ndi zolungama,Ndiponso kuti mwandilanga chifukwa chakuti ndinu wokhulupirika.  76  Kukoma mtima kwanu kosatha kundilimbikitse,Monga mwa mawu anu kwa ine mtumiki wanu.+  77  Ndisonyezeni chifundo chanu kuti ndikhalebe ndi moyo,+Pakuti ndimakonda chilamulo chanu.+  78  Odzikuza achite manyazi, chifukwa andisocheretsa popanda chifukwa,+Koma ine ndimasinkhasinkha malamulo anu.+  79  Anthu okuopani abwerere kwa ine,+Chimodzimodzinso odziwa zikumbutso zanu.+  80  Mtima wanga usunge malangizo anu mosalakwitsa kanthu,Kuti ndisachite manyazi. כ [Kaph]  81  Ine ndafooka chifukwa cholakalaka chipulumutso chanu,+Pakuti ndayembekezera mawu anu.+  82  Maso anga alefuka chifukwa cholakalaka mawu anu,+Ndipo ndikunena kuti: “Kodi mudzandilimbikitsa liti?”+  83  Ndakhala ngati thumba lachikopa mu utsi,Koma sindinaiwale malangizo anu.  84  Kodi ine mtumiki wanu ndidikira kufikira liti?+Kodi anthu ondizunza mudzawaweruza liti?+  85  Anthu amene sachita zinthu mogwirizana ndi chilamulo chanu,+Anthu odzikuza akumba mbuna kuti andigwire.+  86  Malamulo anu onse ndi odalirika.Odzikuza andizunza popanda chifukwa. Chonde, ndithandizeni.+  87  Iwo anangotsala pang’ono kundifafaniza padziko lapansi,Koma ine sindinasiye malamulo anu.  88  Ndisungeni wamoyo monga mwa kukoma mtima kwanu kosatha,+Kuti ndisunge zikumbutso zotuluka pakamwa panu.+ ל [Laʹmedh]  89  Inu Yehova, mawu anu anakhazikika kumwamba,+Mpaka kalekale.+  90  Kukhulupirika kwanu kudzakhalapobe ku mibadwomibadwo.Mwakhazikitsa mwamphamvu dziko lapansi, kuti lisagwedezeke.+  91  Chilengedwe chonse chakhalapobe kufikira lero chifukwa cha zigamulo zanu,+Pakuti chilengedwe chonse chimakutumikirani.  92  Ndikanapanda kukonda chilamulo chanu,+Ndikanatheratu m’masautso anga.+  93  Sindidzaiwala malamulo anu mpaka kalekale,+Chifukwa mwandisungabe wamoyo kudzera m’malamulo amenewo.  94  Ine ndine wanu. Chonde ndipulumutseni,Chifukwa ndaphunzira malamulo anu ndi kuwasunga.+  95  Oipa amandiyembekezera kuti andiwononge,Koma ine ndimamvetsera zikumbutso zanu.+  96  Ndaona kuti zinthu zonse zabwino kwambiri zili ndi malire.Koma malamulo anu amakhudza mbali zonse. מ [Mem]  97  Ndimakonda kwambiri chilamulo chanu!+Ndimasinkhasinkha chilamulocho tsiku lonse.+  98  Malamulo anu amandichititsa kukhala wanzeru kuposa adani anga,Chifukwa ndi anga mpaka kalekale.  99  Ndakhala wozindikira kwambiri kuposa aphunzitsi anga,+Chifukwa ndimasinkhasinkha zikumbutso zanu.+ 100  Ndimachita zinthu mozindikira kuposa anthu achikulire,Chifukwa ndimasunga malamulo anu.+ 101  Ndaletsa mapazi anga kuyenda m’njira iliyonse yoipa.+Ndachita izi kuti ndisunge mawu anu.+ 102  Sindinapatuke pa zigamulo zanu,Pakuti inu mwandilangiza. 103  Mawu anu amatsekemera m’kamwa mwanga,Kuposa mmene uchi umakomera!+ 104  Chifukwa cha malamulo anu ndimachita zinthu mozindikira.+N’chifukwa chake ndimadana ndi njira iliyonse yachinyengo.+ נ [Nun] 105  Mawu anu ndi nyale younikira kumapazi anga,Ndi kuwala kounikira njira yanga.+ 106  Ndalumbira kuti ndidzasunga zigamulo zanu zolungama,Ndipo ndidzakwaniritsa lumbiro langa. 107  Ndasautsika kwambiri.+Inu Yehova, ndisungenibe wamoyo monga mwa mawu anu.+ 108  Inu Yehova, chonde kondwerani ndi nsembe zaufulu za pakamwa panga,Ndipo ndiphunzitseni zigamulo zanu. 109  Moyo wanga uli pangozi nthawi zonse,*Koma sindinaiwale chilamulo chanu.+ 110  Oipa anditchera msampha,+Koma ine sindinasochere ndi kuchoka pa malamulo anu.+ 111  Ndatenga zikumbutso zanu kukhala chuma changa mpaka kalekale,+Pakuti zimakondweretsa mtima wanga.+ 112  Ndatsimikiza mtima kutsatira malangizo anu,Mpaka kalekale, ndithu kwa moyo wanga wonse.+ ס [Saʹmekh] 113  Ndimadana ndi anthu amitima iwiri,Koma ndimakonda chilamulo chanu.+ 114  Inu ndinu malo anga obisalamo ndi chishango changa,+Pakuti ndayembekezera mawu anu.+ 115  Ndichokereni anthu ochita zoipa inu,+Kuti ndisunge malamulo a Mulungu wanga. 116  Inu Mulungu, ndithandizeni monga mwa mawu anu kuti ndikhalebe ndi moyo,+Ndipo musandichititse manyazi chifukwa cha chiyembekezo changa.+ 117  Ndithandizeni kuti ndipulumutsidwe,+Ndipo ndidzamvera malangizo anu nthawi zonse. 118  Onse osochera ndi kuchoka pa malangizo anu mwawataya kutali,Pakuti ndi achinyengo komanso onama.+ 119  Anthu onse oipa mwawachotsa padziko lapansi ngati zonyansa.*N’chifukwa chake ine ndimakonda zikumbutso zanu.+ 120  Chifukwa choopa inu, thupi langa linagwidwa nthumanzi,Ndipo chifukwa cha zigamulo zanu, ndinachita mantha. ע [ʽAʹyin] 121  Ndapereka ziweruzo zolungama ndipo ndachita zinthu mwachilungamo.Musandipereke kwa anthu ondichitira chinyengo.+ 122  Khalani ngati chikole kwa ine mtumiki wanu kuti mudzandichitira zabwino.Anthu odzikuza asandichitire chinyengo.+ 123  Maso anga afooka chifukwa cholakalaka chipulumutso chanu+Ndi mawu anu olungama.+ 124  Ndichitireni zabwino ine mtumiki wanu monga mwa kukoma mtima kwanu kosatha,+Ndipo ndiphunzitseni malamulo anu.+ 125  Ine ndine mtumiki wanu.+ Ndithandizeni kukhala wozindikira,Kuti ndidziwe zikumbutso zanu.+ 126  Ino ndi nthawi yakuti inu Yehova muchitepo kanthu,+Chifukwa anthu odzikuzawo aphwanya chilamulo chanu. 127  N’chifukwa chake ine ndimakonda malamulo anu+Kuposa golide, golide woyenga bwino.+ 128  Choncho ndaona kuti malamulo anu onse okhudza chilichonse ndi olungama.+Ndimadana ndi njira iliyonse yachinyengo.+ פ [Peʼ] 129  Zikumbutso zanu n’zodabwitsa.+N’chifukwa chake ine ndimazisunga.+ 130  Kuululidwa kwa mawu anu kumapereka kuwala,+Kumathandiza anthu osadziwa zambiri kukhala ozindikira.+ 131  Ndatsegula kwambiri pakamwa panga kuti ndipume mofulumira,+Chifukwa ndikulakalaka malamulo anu.+ 132  Ndicheukireni ndi kundikomera mtima,Mogwirizana ndi zigamulo zimene mumapereka kwa anthu okonda dzina lanu.+ 133  Mwapondetsa mwamphamvu mapazi anga pa mawu anu,+Ndipo musalole kuti choipa chilichonse chindilamulire.+ 134  Ndiwomboleni kwa munthu aliyense wondichitira zachinyengo,+Ndipo ine ndidzasunga malamulo anu.+ 135  Ndikomereni mtima ine mtumiki wanu,Ndipo ndiphunzitseni malamulo anu. 136  Misozi yatsika m’maso mwanga ngati mitsinje ya madzi,Chifukwa chakuti iwo sanasunge chilamulo chanu.+ צ [Tsa·dhehʹ] 137  Ndinu wolungama inu Yehova,Ndipo zigamulo zanu ndi zowongoka. 138  M’chilungamo chanu ndiponso kukhulupirika kwanu kosaneneka+Mwatilamula kuti tisunge zikumbutso zanu.+ 139  Changu changa chandidya,Chifukwa adani anga aiwala mawu anu.+ 140  Mawu anu ndi oyengeka kwambiri,Ndipo ine mtumiki wanu ndimawakonda.+ 141  Kwa ena ndine wopanda pake ndi wonyozeka.+Koma sindinaiwale malamulo anu.+ 142  Chilungamo chanu ndi chilungamo mpaka kalekale,+Ndipo chilamulo chanu ndi choonadi. 143  Zowawa ndi zovuta zinandigwera.+Koma ndinakonda malamulo anu.+ 144  Zikumbutso zanu zidzakhalabe zolungama mpaka kalekale.+Ndithandizeni kukhala wozindikira kuti ndikhalebe ndi moyo.+ ק [Qohph] 145  Ndaitana ndi mtima wanga wonse.+ Ndiyankheni inu Yehova.+Ndidzasunga malangizo anu. 146  Ndakuitanani. Ndipulumutseni chonde!+Ndidzasunga zikumbutso zanu.+ 147  Ndadzuka m’mawa kuli mbuu,+ kuti ndipemphe thandizo kwa inu,+Pakuti ndayembekezera mawu anu.+ 148  Ndimadzuka pa ulonda wa usiku,+Kuti ndisinkhesinkhe mawu anu.+ 149  Imvani mawu anga mwa kukoma mtima kwanu kosatha.+Inu Yehova, ndisungenibe wamoyo mogwirizana ndi zigamulo zanu.+ 150  Okonda kuchita khalidwe lotayirira abwera pafupi ndi ine.Iwo atalikirana kwambiri ndi chilamulo chanu. 151  Inu Yehova muli pafupi,Ndipo malamulo anu onse ndi choonadi. 152  Zina mwa zikumbutso zanu ndinazidziwa kale kwambiri,+Pakuti munazikhazikitsa kalekale.+ ר [Rehsh] 153  Onani kusautsika kwanga ndipo ndipulumutseni,+Pakuti sindinaiwale chilamulo chanu.+ 154  Ndiyankhireni mlandu wanga ndi kundipulumutsa.Ndisungeni wamoyo mogwirizana ndi mawu anu.+ 155  Chipulumutso chili kutali ndi anthu oipa,+Pakuti sanaphunzire malamulo anu ndi kuwasunga. 156  Chifundo chanu n’chachikulu, inu Yehova.Ndisungenibe wamoyo mogwirizana ndi zigamulo zanu.+ 157  Anthu ondizunza komanso adani anga ndi ambiri.+Koma ine sindinapatuke pa zikumbutso zanu.+ 158  Ndaona anthu ochita zinthu mwachinyengo,Ndipo amandinyansa chifukwa sasunga mawu anu.+ 159  Onani kuti ndimakonda malamulo anu.+Inu Yehova, ndisungenibe wamoyo mwa kukoma mtima kwanu kosatha.+ 160  Mawu anu onse ndi choonadi chokhachokha,Ndipo chigamulo chanu chilichonse cholungama chidzakhalapo mpaka kalekale.+ ש [Sin] kapena kuti [Shin] 161  Akalonga andizunza popanda chifukwa,Koma mtima wanga umaopa mawu anu. 162  Ndikukondwera chifukwa cha mawu anu,+Monga mmene munthu amachitira akapeza zofunkha zambiri. 163  Ndimadana ndi chinyengo+ ndipo chimandinyansa,+Koma ndimakonda chilamulo chanu.+ 164  Ndimakutamandani maulendo 7 pa tsiku,+Chifukwa cha zigamulo zanu zolungama.+ 165  Okonda chilamulo chanu amapeza mtendere wochuluka,+Ndipo palibe chowakhumudwitsa.+ 166  Ndayembekezera chipulumutso chanu, inu Yehova,Ndipo ndatsatira malamulo anu. 167  Ndasunga zikumbutso zanu,+Ndipo ndimazikonda kwambiri.+ 168  Ndasunga malamulo anu ndi zikumbutso zanu,+Pakuti njira zanga zonse zili pamaso panu.+ ת [Taw] 169  Inu Yehova, imvani kulira kwanga kochonderera.+Ndithandizeni kuti ndikhale wozindikira, monga mwa mawu anu. 170  Pempho langa lakuti mundichitire chifundo lifike kwa inu.+Ndipulumutseni monga mwa mawu anu. 171  Milomo yanga itulutse mawu okutamandani,+Pakuti mwandiphunzitsa malamulo anu. 172  Lilime langa liimbe za mawu anu,+Pakuti malamulo anu onse ndi olungama.+ 173  Dzanja lanu lindithandize,+Chifukwa ndasankha malamulo anu. 174  Ndikulakalaka chipulumutso chanu, inu Yehova,Ndipo ndimakonda kwambiri chilamulo chanu.+ 175  Ndisungenibe wamoyo kuti ndikutamandeni,+Zigamulo zanu zindithandize. 176  Ndayendayenda ngati nkhosa yosochera.+ Ndifunefuneni ine mtumiki wanu,Pakuti sindinaiwale malamulo anu.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “phindu lopezeka mwachinyengo pamalonda.”
Mawu ake enieni, “ndafewetsa nkhope yanu.”
Mawu ake enieni, “moyo wanga uli m’dzanja langa.”
Zimenezi ndi zonyansa zotsalira poyenga zitsulo.