Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 118:1-29

118  Yamikani Yehova anthu inu, pakuti iye ndi wabwino.+ Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe  mpaka kalekale.+   Tsopano Isiraeli anene kuti: “Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.”+   A nyumba ya Aroni anene kuti:+ “Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.”+   Oopa Yehova anene kuti:+ “Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.”+   M’masautso anga ndinaitana Ya.+ Ya anandiyankha ndi kundiika pamalo otakasuka.+   Yehova ali kumbali yanga, sindidzaopa.+ Munthu wochokera kufumbi angandichite chiyani?+   Yehova ali kumbali yanga pamodzi ndi anthu amene akundithandiza,+ Ndipo ine ndidzayang’ana anthu odana nane atagonja.+   Kuthawira kwa Yehova n’kwabwino+ Kusiyana ndi kudalira munthu wochokera kufumbi.+   Kuthawira kwa Yehova n’kwabwino+ Kusiyana ndi kudalira anthu olemekezeka.+ 10  Mitundu yonse ya anthu inandizungulira,+ Koma ndinali kuikankhira kutali m’dzina la Yehova.+ 11  Mitunduyo inandizungulira, ndithu inandizungulira kumbali zonse.+ Koma ndinali kuikankhira kutali m’dzina la Yehova. 12  Inandizungulira ngati njuchi,+ Koma inazima ngati moto wa zitsamba zaminga.+ Ndinali kuikankhira kutali m’dzina la Yehova.+ 13  Munandikankha kwambiri kuti ndigwe,+ Koma Yehova anandithandiza.+ 14  Ya ndiye malo anga obisalapo ndi mphamvu zanga,+ Iye amandipulumutsa.+ 15  M’mahema+ a olungama+ Mumamveka mfuu yachisangalalo ndipo muli chipulumutso.+ Dzanja lamanja la Yehova limachita zamphamvu.+ 16  Dzanja lamanja la Yehova likudzikweza pamwamba.+ Dzanja lamanja la Yehova limachita zamphamvu.+ 17  Sindidzafa, koma ndidzakhalabe ndi moyo,+ Kuti ndilengeze ntchito za Ya.+ 18  Ya anandilanga mwamphamvu,+ Koma sanandipereke ku imfa.+ 19  Nditsegulireni zipata zachilungamo,+ anthu inu. Ndidzalowamo ndipo ndidzatamanda Ya.+ 20  Ichi ndi chipata cha Yehova.+ Olungama adzalowamo.+ 21  Ndidzakutamandani, chifukwa munandiyankha+ Ndi kundipulumutsa.+ 22  Mwala umene omanga nyumba anaukana+ Wakhala mwala wofunika kwambiri wapakona.+ 23  Umenewu wachokera kwa Yehova,+ Ndipo ndi wodabwitsa m’maso mwathu.+ 24  Ili ndi tsiku limene Yehova wapanga.+ Tidzakondwera ndi kusangalala pa tsiku limeneli.+ 25  Haa! Inu Yehova, chonde tipulumutseni.+ Haa! Inu Yehova, chonde tithandizeni kuti zinthu zitiyendere bwino.+ 26  Wodala ndi Iye wobwera m’dzina la Yehova.+ Takudalitsani anthu inu potuluka m’nyumba ya Yehova.+ 27  Yehova ndiye Mulungu,+ Ndipo amatipatsa kuwala.+ Kongoletsani gulu la anthu amene ali pachikondwerero+ ndi nthambi za mitengo,+ anthu inu. Likongoletseni mpaka kukafika panyanga za guwa lansembe.+ 28  Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakutamandani.+ Ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakukwezani.+ 29  Yamikani Yehova anthu inu, pakuti iye ndi wabwino.+ Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

Mawu a M'munsi