Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 116:1-19

116  Mtima wanga ndi wodzaza ndi chikondi, chifukwa Yehova amamva+ Mawu anga ndi madandaulo anga.+   Pakuti watchera khutu lake kwa ine,+ Ndipo ndidzaitanira pa iye masiku onse a moyo wanga.+   Zingwe za imfa zinandizungulira+ Ndipo ndinasautsika ngati kuti ndili m’Manda.+ Ndinapitiriza kusautsika ndi kukhala wachisoni,+   Koma ndinaitana pa dzina la Yehova kuti:+ “Inu Yehova, pulumutsani moyo wanga!”+   Yehova ndi wachisomo ndi wolungama.+ Mulungu wathu amasonyeza chifundo.+   Yehova amateteza anthu osadziwa zambiri.+ Ndinali wosautsika koma iye anandipulumutsa.+   Iwe moyo wanga, bwerera kumalo ako ampumulo,+ Pakuti Yehova wakuchitira zinthu zabwino.+   Pakuti inu mwapulumutsa moyo wanga ku imfa,+ Mwateteza maso anga kuti asakhetse misozi ndiponso phazi langa kuti lisapunthwe.+   Ndidzayenda+ pamaso pa Yehova m’dziko la anthu amoyo.+ 10  Ndinali ndi chikhulupiriro,+ n’chifukwa chake ndinalankhula.+ Ndinali kusautsika kwambiri. 11  Pamene ndinapanikizika ndinati:+ “Munthu aliyense ndi wabodza.”+ 12  Yehova ndidzamubwezera chiyani+ Pa zabwino zonse zimene wandichitira?+ 13  Ndidzamwa za m’kapu yachipulumutso chachikulu,+ Ndipo ndidzaitana pa dzina la Yehova.+ 14  Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova,+ Pamaso pa anthu ake onse. 15  M’maso mwa Yehova Imfa ya anthu ake okhulupirika ndi nkhani yaikulu.+ 16  Inu Yehova,+ Inetu ndine mtumiki wanu.+ Ndine mtumiki wanu, mwana wa kapolo wanu wamkazi.+ Mwamasula zingwe zimene anandimanga nazo.+ 17  Ndidzapereka nsembe zoyamikira kwa inu,+ Ndipo ndidzaitana pa dzina la Yehova.+ 18  Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova,+ Ndidzawakwaniritsa pamaso pa anthu ake onse,+ 19  M’mabwalo a nyumba ya Yehova,+ Pakati pa iwe Yerusalemu.+ Tamandani Ya, anthu inu!+

Mawu a M'munsi