Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 115:1-18

115  Ife sitikuyenerera kalikonse, inu Yehova, ife sitikuyenerera kalikonse,+ Koma dzina lanu ndi loyenera kulemekezedwa+ Malinga ndi kukoma mtima kwanu kosatha, malinganso ndi choonadi chanu.+   Musalole kuti mitundu izinena kuti:+ “Mulungu wawo ali kuti tsopano?”+   Koma Mulungu wathu ali kumwamba.+ Chilichonse chimene anafuna kuchita anachita.+   Mafano awo ndi opangidwa ndi siliva ndi golide,+ Ntchito ya manja a munthu wochokera kufumbi.+   Pakamwa ali napo koma salankhula,+ Maso ali nawo koma saona.+   Makutu ali nawo koma satha kumva.+ Mphuno ali nayo koma sanunkhiza.+   Manja ali nawo, koma sakhudza kanthu.+ Mapazi ali nawo koma sayenda.+ Satulutsa mawu ndi mmero wawo.+   Amene amawapanga adzafanana nawo.+ Onse amene amawakhulupirira adzakhala ngati mafanowo.+   Iwe Isiraeli, khulupirira Yehova.+ Iye ndiye thandizo lako ndi chishango chako.+ 10  Inu nyumba ya Aroni, khulupirirani Yehova.+ Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.+ 11  Inu oopa Yehova, khulupirirani Yehova.+ Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.+ 12  Yehova watikumbukira, ndipo adzapereka madalitso,+ Adzadalitsa nyumba ya Isiraeli,+ Adzadalitsa nyumba ya Aroni.+ 13  Yehova adzadalitsa anthu omuopa,+ Adzadalitsa onsewo osasiyapo aliyense.+ 14  Yehova adzakuchulukitsani,+ Inu ndi ana anu.+ 15  Inu ndinu amene mwadalitsidwa ndi Yehova,+ Wopanga kumwamba ndi dziko lapansi.+ 16  Kunena za kumwamba, kumwamba ndi kwa Yehova,+ Koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.+ 17  Akufa satamanda Ya,+ Ngakhalenso aliyense wotsikira kuli chete.+ 18  Koma ife tidzatamanda Ya+ Kuyambira tsopano mpaka kalekale.+ Tamandani Ya, anthu inu!+

Mawu a M'munsi