Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 114:1-8

114  Pamene Isiraeli anatuluka mu Iguputo,Pamene nyumba ya Yakobo inatuluka pakati pa anthu olankhula zosamveka,   Yuda anakhala malo ake oyera,Ndipo Isiraeli anakhala ufumu wake waukulu.   Nyanja inaona ndipo inathawa.Yorodano anabwerera m’mbuyo.   Mapiri anadumphadumpha ngati nkhosa zamphongo,Zitunda zinadumphadumpha ngati ana a nkhosa.   Kodi chinavuta n’chiyani nyanja iwe kuti uthawe?Kodi iwe Yorodano chinavuta n’chiyani kuti ubwerere m’mbuyo?   Nanga inu mapiri, chinavuta n’chiyani kuti mudumphedumphe ngati nkhosa zamphongo?+Inunso zitunda, chinavuta n’chiyani kuti mudumphedumphe ngati ana a nkhosa?+   Chifukwa cha Ambuye, chita mantha aakulu dziko lapansi iwe,Chita mantha aakulu chifukwa cha Mulungu wa Yakobo,   Amene amasintha thanthwe kukhala dambo la madzi,Ndiponso amasintha mwala wa nsangalabwi kukhala kasupe.

Mawu a M'munsi