Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 113:1-9

113  Tamandani Ya, anthu inu!Inu atumiki a Yehova, mutamandeni,+Tamandani dzina la Yehova.+   Dzina la Yehova lidalitsike,Kuyambira tsopano mpaka kalekale.   Kuyambira kotulukira dzuwa mpaka kumene limalowera,+Dzina la Yehova liyenera kutamandidwa.   Yehova wakwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.+Ulemerero wake uli pamwamba pa kumwamba.   Ndani angafanane ndi Yehova Mulungu wathu,Amene amakhala pamwamba?   Iye amatsika m’munsi kuti aone kumwamba ndi dziko lapansi.+   Amadzutsa munthu wonyozeka kumuchotsa m’fumbi.+Amakweza munthu wosauka kumuchotsa padzala,   Kuti amukhazike pamodzi ndi anthu olemekezeka,Pamodzi ndi anthu olemekezeka pakati pa anthu a Mulungu.+   Akuchititsa mkazi wosabereka kukhala m’nyumbaMonga mayi wosangalala wa ana aamuna.+Tamandani Ya, anthu inu!+

Mawu a M'munsi