Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Masalimo 112:1-10

112  Tamandani Ya, anthu inu!+ א [ʼA′leph]Wodala ndi munthu woopa Yehova,+ב [Behth]Munthu amene amasangalala kwambiri+ ndi malamulo ake.+ ג [Gi′mel]   Ana ake adzakhala amphamvu padziko lapansi.+ ד [Da′leth]Ndipo m’badwo wa anthu olungama udzadalitsidwa.+ ה [Heʼ]   Zinthu zamtengo wapatali ndiponso chuma zili m’nyumba yake,+ו [Waw]Ndipo chilungamo chake chidzakhalapo kwamuyaya.+ ז [Za′yin]   Waunika mu mdima kuti anthu owongoka mtima aone kuwala.+ ח [Chehth]Iye ndi wachisomo, wachifundo ndi wolungama.+ ט [Tehth]   Munthu wachisomo+ komanso wokongoza ena zinthu ndi wabwino.+ י [Yohdh]Amachita zinthu mwachilungamo.+ כ [Kaph]   Ndithudi munthu wotero sadzagwedezeka ngakhale pang’ono.+ ל [La′medh]Wolungama adzakumbukiridwa mpaka kalekale.+ מ [Mem]   Sadzaopa uthenga woipa.+ נ [Nun]Mtima wake ndi wokhazikika,+ ndipo umadalira Yehova.+ ס [Sa′mekh]   Mtima wake sungagwedezeke,+ ndipo sadzachita mantha,+ע [ʽA′yin]Pamapeto pake adzayang’ana adani ake atagonjetsedwa.+ פ [Peʼ]   Iye wagawira ena mowolowa manja, wapereka kwa anthu aumphawi.+ צ [Tsa·dheh′]Chilungamo chake chidzakhalapo kwamuyaya.+ ק [Qohph]Nyanga* yake idzakwezedwa ndi ulemerero.+ ר [Rehsh] 10  Woipa adzaona zimenezi ndipo adzasautsika.+ ש [Shin]Adzakukuta mano ndi kusungunuka.+ ת [Taw]Chikhumbo cha anthu oipa chidzatha.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa 1Sa 2:1.