Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Masalimo 111:1-10

111  Tamandani Ya, anthu inu!+ א [ʼA′leph]Ndidzatamanda Yehova ndi mtima wanga wonse,+ב [Behth]Pakati pa gulu+ la owongoka mtima ndi pamsonkhano wawo.+ ג [Gi′mel]   Ntchito za Yehova ndi zazikulu,+ד [Da′leth]Onse amene amasangalala nazo amazisinkhasinkha.+ ה [Heʼ]   Zochita zake+ n’zaulemerero ndi ulemu,+ו [Waw]Ndipo chilungamo chake chidzakhalapobe kwamuyaya.+ ז [Za′yin]   Iye wakonza zoti ntchito zake zodabwitsa zizikumbukiridwa.+ ח [Chehth]Yehova ndi wachisomo ndiponso wachifundo.+ ט [Tehth]   Wapereka chakudya kwa anthu omuopa.+ י [Yohdh]Iye adzakumbukira pangano lake nthawi zonse.+ כ [Kaph]   Wafotokozera anthu ake mphamvu za ntchito zake,+ל [La′medh]Mwa kuwapatsa cholowa cha mitundu ina ya anthu.+ מ [Mem]   Ntchito za manja ake zimadziwika ndi choonadi ndiponso chiweruzo.+נ [Nun]Malamulo onse amene amapereka ndi odalirika.+ ס [Sa′mekh]   Ndi ochirikizika bwino mpaka muyaya, ndithu mpaka kalekale,+ע [ʽA′yin]Ndipo amawapereka m’choonadi ndiponso molungama.+ פ [Peʼ]   Wawombola anthu ake.+ צ [Tsa·dheh′]Wakhazikitsa pangano lake mpaka kalekale.+ ק [Qohph]Dzina lake ndi loyera ndi lochititsa mantha.+ ר [Rehsh] 10  Chiyambi cha nzeru ndicho kuopa Yehova.+ ש [Sin]Onse otsatira malamulo a Mulungu ndi ozindikira.+ ת [Taw]Iye ayenera kutamandidwa mpaka muyaya.+

Mawu a M'munsi