Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 110:1-7

Salimo la Davide. 110  Yehova wauza Ambuye wanga kuti:+ “Khala kudzanja langa lamanja+ Kufikira nditaika adani ako monga chopondapo mapazi ako.”+   Yehova adzatambasula ndodo+ yako yachifumu yamphamvu kuchokera m’Ziyoni+ ndi kunena kuti: “Pita ukagonjetse anthu pakati pa adani ako.”+   Anthu ako+ adzadzipereka mofunitsitsa+ pa tsiku limene udzatsogolera asilikali ako kunkhondo.+ Wadzikongoletsa ndi ulemerero,+ Ndipo gulu la achinyamata amene ali ngati mame a m’bandakucha lili pamodzi ndi iwe.+   Yehova walumbira+ (ndipo sadzasintha maganizo). Iye wati:+ “Iwe ndiwe wansembe mpaka kalekale,+ Monga mwa unsembe wa Melekizedeki!”+   Yehova amene ali kudzanja lako lamanja+ Adzaphwanyaphwanya mafumu pa tsiku la mkwiyo wake.+   Adzapereka chiweruzo pakati pa anthu a mitundu ina.+ Adzachititsa mitembo ya anthu kupezeka paliponse.+ Adzaphwanyaphwanya mtsogoleri wa dziko la anthu ambiri.+   Panjira, adzamwa madzi a m’chigwa.+ N’chifukwa chake adzatukula kwambiri mutu wake.+

Mawu a M'munsi