Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 11:1-7

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide. 11  Ine ndathawira kwa Yehova.+ Kodi mulibe mantha? Mukundiuza kuti: “Thawirani kumapiri anu ngati mbalame!+   Pakuti oipa akunga uta,+ Akonzekeretsa mivi yawo kuti aiponye ndi uta, Kuti alase anthu owongoka mtima kuchokera pamalo amdima.+   Kodi munthu wolungama angachite chiyani Maziko achilungamo atagumulidwa?”+   Yehova ali m’kachisi wake wopatulika.+ Yehova, mpando wake wachifumu uli kumwamba.+ Maso ake amaona, maso ake owala amasanthula+ ana a anthu.   Yehova amasanthula anthu olungama ndi oipa omwe,+ Ndipo Mulungu amadana kwambiri ndi aliyense wokonda chiwawa.+   Iye adzavumbitsira oipa misampha, moto ndi sulufule,+ Komanso mphepo yotentha, monga gawo limene ayenera kumwa.+   Pakuti Yehova ndi wolungama.+ Amakonda ntchito zolungama.+ Anthu owongoka mtima ndi amene adzaona nkhope yake.+

Mawu a M'munsi