Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 109:1-31

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la Davide. 109  Inu Mulungu amene ndimakutamandani,+ musakhale chete.+   Munthu woipa ndiponso munthu wachinyengo andinenera zoipa ndi pakamwa pawo.+ Iwo anena za ine ndi lilime lonama.+   Andizungulira ndi mawu achidani,+ Ndipo akulimbana nane popanda chifukwa.+   Ndikawasonyeza chikondi amanditsutsa,+ Koma ine ndimapemphera.+   Ndikawachitira zabwino amandibwezera zoipa,+ Ndikawasonyeza chikondi amandibwezera chidani.+   Muikireni woweruza woipa, Ndipo kudzanja lake lamanja kuime wotsutsana naye.+   Pamene akuweruzidwa amuweruze kuti ndi woipa. Ndipo pemphero lake likhale tchimo.+   Masiku a moyo wake akhale ochepa.+ Udindo wake monga woyang’anira utengedwe ndi munthu wina.+   Ana ake akhale amasiye,*+ Ndipo mkazi wakenso akhale wamasiye.+ 10  Ana ake azingoyendayenda ndithu,+ Ndipo azipemphapempha. Azichoka m’mabwinja mmene akukhala, n’kupita kukafunafuna chakudya.+ 11  Wopereka ngongole yakatapira* atchere msampha pa zonse zimene ali nazo,+ Ndipo anthu achilendo+ afunkhe zinthu zimene wakhetsera thukuta.+ 12  Pasapezeke womusonyeza kukoma mtima kosatha,+ Ndipo pasapezeke wokomera mtima ana ake amasiyewo. 13  Mbadwa zake ziphedwe ndi kuchotsedwa m’dziko.+ Dzina lawo lifafanizidwe mu m’badwo wotsatira.+ 14  Yehova akumbukire cholakwa cha makolo ake,+ Ndipo tchimo la mayi ake+ lisafafanizidwe.+ 15  Tchimo ndi cholakwacho zikhale pamaso pa Yehova nthawi zonse,+ Ndipo achotse dzina lawo padziko lapansi kuti lisakumbukiridwenso,+ 16  Chifukwa chakuti sanakumbukire kusonyeza kukoma mtima kosatha,+ M’malomwake anapitiriza kuthamangitsa wosautsika ndi wosauka,+ Komanso munthu wa mtima wachisoni kuti amuphe.+ 17  Iye anakonda kutemberera ena,+ mwakuti matemberero anabwera kwa iye.+ Koma kudalitsa ena sikunali kumusangalatsa,+ Moti madalitso anali patali ndi iye,+ 18  Iye anali kuvala matemberero ngati chovala.+ Matembererowo analowa mwa iye ngati madzi,+ Ndiponso analowa m’mafupa ake ngati mafuta. 19  Kwa iye matembererowo akhale ngati chovala chimene amadziphimba nacho,+ Komanso ngati lamba amene amamanga m’chiuno mwake nthawi zonse.+ 20  Amenewa ndi malipiro a Yehova kwa aliyense amene amalimbana nane,+ Ndi kwa amene amakamba zondichitira zinthu zoipa.+ 21  Koma inu ndinu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa.+ Ndikomereni mtima chifukwa cha dzina lanu.+ Ndilanditseni,+ popeza kukoma mtima kwanu kosatha ndi kwakukulu. 22  Ine ndasautsika ndipo ndasauka,+ Mtima wanga walasika mkati mwanga.+ 23  Ine ndiyenera kuchoka mofanana ndi chithunzithunzi chimene chimazimiririka dzuwa likalowa.+ Ndakutumulidwa ngati dzombe. 24  Mawondo anga akugwedezeka chifukwa chosala kudya,+ Ndawonda ndipo ndilibe mafuta alionse odzola.+ 25  Kwa iwo ndakhala chinthu choyenera kutonzedwa.+ Akandiona amapukusa mitu yawo.+ 26  Ndithandizeni, inu Yehova Mulungu wanga.+ Ndipulumutseni malinga ndi kukoma mtima kwanu kosatha.+ 27  Iwo adziwe kuti ili ndi dzanja lanu.+ Adziwe kuti inu Yehova mwachita zimenezi.+ 28  Alekeni anditemberere,+ Koma inu mundipatse madalitso.+ Iwo aimirira kuti andiukire koma inu muwachititse manyazi,+ Ndipo ine mtumiki wanu ndisangalale.+ 29  Amene akulimbana ndi ine avale manyazi,+ Ndipo adziphimbe ndi manyaziwo ngati akudziphimba ndi malaya akunja odula manja.+ 30  Ndidzatamanda kwambiri Yehova ndi pakamwa panga,+ Ndipo ndidzamutamanda pakati pa anthu ambiri.+ 31  Pakuti adzaima kudzanja lamanja la munthu wosauka,+ Kuti am’pulumutse kwa omuweruza mopanda chilungamo.

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “ana aamuna opanda bambo.”
Onani mawu a m’munsi pa Eks 22:25.