Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 108:1-13

Nyimbo ndi Salimo la Davide. 108  Mtima wanga wakhazikika, Inu Mulungu,+ Ndidzaimba nyimbo zokutamandani,+ Mtima wanga udzachitanso chimodzimodzi.+   Iwe choimbira cha zingwe, galamuka, ndi iwenso zeze.+ Ndidzadzuka m’bandakucha usanafike.+   Ndidzakutamandani pakati pa mitundu ya anthu, inu Yehova.+ Ndidzaimba nyimbo zokutamandani pakati pa mitundu ya anthu.+   Pakuti kukoma mtima kwanu kosatha n’kwakukulu ndipo kwafika kumwamba,+ Choonadi chanu chafika kuthambo.+   Inu Mulungu, kwezekani kupitirira kumwamba.+ Ulemerero wanu ukhale pamwamba pa dziko lonse lapansi.+   Kuti okondedwa anu apulumutsidwe,+ Tipulumutseni ndi dzanja lanu lamanja ndi kundiyankha.+   Pokhala woyera, Mulungu walankhula kuti:+ “Ndidzakondwa ndi kupereka Sekemu+ ngati gawo la cholowa.+ Ndipo ndidzayezera anthu anga chigwa cha Sukoti.+   Giliyadi+ ndi wanga ndipo Manase+ ndi wanganso. Efuraimu ndi malo otetezeka a mtsogoleri amene ine ndamuika.+ Yuda ndi ndodo yanga ya mtsogoleri wa asilikali.+   Mowabu+ ndi beseni langa losambiramo.+ Ndidzaponyera Edomu+ nsapato zanga.+ Ndidzafuula mosangalala+ chifukwa chogonjetsa Filisitiya.”+ 10  Ndani adzandibweretsa kumzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri?+ Ndani adzanditsogolera mpaka kukafika ku Edomu?+ 11  Ndinu Mulungu amene mungatichititse kupambana! Koma onani tsopano mwatitaya,+ Ndipo inu Mulungu wathu, simukupita kunkhondo pamodzi ndi magulu athu ankhondo.+ 12  Tithandizeni kuti tichoke m’masautso,+ Pakuti chipulumutso chochokera kwa munthu wochokera kufumbi n’chopanda pake.+ 13  Ndi thandizo la Mulungu, tidzalandira mphamvu,+ Ndipo Mulungu adzapondereza adani athu.+

Mawu a M'munsi