Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 107:1-43

(Masalimo 107 – 150) 107  Yamikani Yehova anthu inu, pakuti iye ndi wabwino.+ Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe  mpaka kalekale.+   Anthu owomboledwa a Yehova anene zimenezi,+ Anthu amene iye wawawombola m’manja mwa mdani,+   Anthu amene anawasonkhanitsa pamodzi kuchokera m’mayiko osiyanasiyana,+ Kuchokera kotulukira dzuwa kukafika kolowera dzuwa,+ Kuchokera kumpoto kukafika kum’mwera.+   Iwo anayendayenda m’chipululu+ mopanda kanthu.+ Sanapeze njira iliyonse yopita kumzinda woti azikhalamo.+   Anali ndi njala komanso ludzu.+ Anafooka kwambiri, kutsala pang’ono kufa.+   Iwo anapitiriza kufuulira Yehova m’masautso awo,+ Ndipo anawalanditsa ku mavuto awo.+   Anawayendetsa m’njira yabwino,+ Kuti akafike kumzinda woti azikhalamo.+   Anthu ayamike Yehova chifukwa cha kukoma mtima kwake kosatha,+ Ndiponso chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa zimene wachitira ana a anthu.+   Pakuti iye wapereka madzi kwa anthu aludzu.+ Ndipo anthu anjala wawadyetsa zinthu zabwino.+ 10  Ena anali kukhala mu mdima, mu mdima wandiweyani,+ Anali akaidi osautsika ndi omangidwa maunyolo,+ 11  Chifukwa anachita zinthu mopandukira+ mawu a Mulungu,+ Ndipo ananyoza malangizo a Wam’mwambamwamba.+ 12  Choncho mwa kuwadzetsera mavuto, Mulungu anagonjetsa mitima yawo.+ Iwo anapunthwa ndipo panalibe wowathandiza.+ 13  Iwo anayamba kuitana Yehova kuti awathandize m’masautso awo,+ Ndipo iye anawapulumutsa ku mavuto awo monga mwa nthawi zonse.+ 14  Iye anawatulutsa mu mdima, mu mdima wandiweyani,+ Ndi kudula zingwe zimene anamangidwa nazo.+ 15  Anthu ayamike Yehova chifukwa cha kukoma mtima kwake kosatha,+ Ndiponso chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa zimene wachitira ana a anthu.+ 16  Pakuti iye wathyola zitseko zamkuwa,+ Ndipo wadula mipiringidzo yachitsulo.+ 17  Anthu amene anali opusa chifukwa cha njira yawo yophwanya malamulo,+ Komanso chifukwa cha zolakwa zawo, pamapeto pake anadzibweretsera masautso.+ 18  Moyo wawo unaipidwa ndi chakudya cha mtundu uliwonse,+ Ndipo anafika pazipata za imfa.+ 19  Iwo anayamba kuitana Yehova kuti awathandize m’masautso awo.+ Ndipo iye anawapulumutsa ku mavuto awo monga mwa nthawi zonse.+ 20  Iye ananena mawu ndipo anawachiritsa,+ Moti anawapulumutsa kudzenje la manda.+ 21  Anthu ayamike Yehova chifukwa cha kukoma mtima kwake kosatha,+ Ndiponso chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa zimene wachitira ana a anthu.+ 22  Iwo apereke nsembe zoyamikira,+ Ndi kulengeza za ntchito zake ndi mfuu yachisangalalo.+ 23  Anthu amene amayenda m’zombo panyanja,+ Amene amachita malonda pamadzi ambiri,+ 24  Amenewa ndi amene aona ntchito za Yehova,+ Ndiponso ntchito zake zodabwitsa m’madzi akuya.+ 25  Aona mmene amautsira mphepo yamkuntho mwa kungonena mawu,+ Moti nyanjayo imachita mafunde.+ 26  Iwo amapita pamwamba, Kenako amatsika pansi. Chifukwa cha masoka, mitima yawo imasungunuka.+ 27  Amadzandira ndipo amayenda peyupeyu ngati munthu woledzera,+ Ndipo ngakhale nzeru zawo zonse zimasokonezeka.+ 28  Iwo amayamba kufuulira Yehova m’masautso awo,+ Ndipo iye amawatulutsa m’mavuto awo.+ 29  Iye amachititsa mphepo yamkuntho kukhala bata,+ Moti mafunde a panyanja amadekha.+ 30  Iwo amasangalala chifukwa mafundewo atha, Ndipo Mulungu amawatsogolera kudoko limene iwo akufuna.+ 31  Anthu ayamike Yehova chifukwa cha kukoma mtima kwake kosatha,+ Ndiponso chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa zimene wachitira ana a anthu.+ 32  Amukweze mumpingo wa anthu,+ Ndipo amutamande  m’bwalo la anthu achikulire.+ 33  Amasandutsa mitsinje kukhala chipululu,+ Ndiponso akasupe a madzi kukhala malo opanda madzi.+ 34  Nthaka yobala zipatso amaisandutsa dziko lamchere,+ Chifukwa cha kuipa kwa anthu okhala mmenemo. 35  Amasandutsa chipululu kukhala dambo la madzi,+ Ndipo dziko lopanda madzi amalisintha kukhala dera la akasupe amadzi.+ 36  Kumeneko amakhazikako anthu anjala,+ Kuti amange mzinda woti azikhalamo.+ 37  Anthuwo amafesa mbewu ndi kulima minda ya mpesa,+ Kuti akhale ndi zokolola.+ 38  Mulungu amawadalitsa moti amachuluka kwambiri,+ Ndipo salola kuti ng’ombe zawo zikhale zochepa.+ 39  Koma iwo amakhalanso ochepa ndipo amawerama,+ Chifukwa cha kuponderezedwa, masoka ndi chisoni.+ 40  Mulungu akutsanulira mnyozo pa anthu olemekezeka,+ Moti iye akuwachititsa kuyendayenda m’chipululu, mmene mulibe njira.+ 41  Koma akuteteza munthu wosauka ku nsautso,+ Ndipo akumuchulukitsa kukhala mabanja ambiri ngati gulu la nkhosa.+ 42  Olungama amaona ndi kukondwera.+ Koma anthu onse osalungama amatseka pakamwa.+ 43  Wanzeru ndani? Iye aona zimenezi,+ Ndi kuchita chidwi ndi ntchito za Yehova zosonyeza kukoma mtima kwake kosatha.+

Mawu a M'munsi