Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 106:1-48

106  Tamandani Ya, anthu inu!+ Yamikani Yehova, chifukwa iye ndi wabwino.+ Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+   Ndani anganene zinthu zamphamvu zimene Yehova wachita,+ Kapena ndani angamutamande mokwanira?+   Odala ndi anthu amene amatsata chilungamo,+ Ndi kuchita zolungama nthawi zonse.+   Ndikumbukireni inu Yehova, ndipo ndisonyezeni kukoma mtima kumene mumasonyeza anthu anu.+ Ndisamalireni ndi kundipulumutsa,+   Kuti ndione ubwino umene mumapereka kwa osankhidwa anu,+ Kuti ndikondwere pamene mtundu wanu ukukondwera,+ Ndiponso kuti ndinyadire pamodzi ndi cholowa chanu.+   Tachimwa mofanana ndi makolo athu.+ Tachita zinthu zosayenera, tachita zinthu zoipa.+   Makolo athu ku Iguputo, Sanasonyeze kuzindikira kulikonse ntchito zanu zodabwitsa.+ Sanakumbukire kuchuluka kwa kukoma mtima kwanu kosatha,+ Koma anapanduka panyanja, pafupi ndi Nyanja Yofiira.+   Koma Mulungu anawapulumutsa chifukwa cha dzina lake,+ Kuti mphamvu zake zidziwike.+   Choncho anadzudzula Nyanja Yofiira, ndipo pang’onopang’ono nyanjayo inauma.+ Pamenepo anawayendetsa kudutsa pakati pa madzi akuya ngati akuwayendetsa m’chipululu.+ 10  Chotero anawapulumutsa m’manja mwa wodana nawo,+ Ndipo anawawombola m’manja mwa mdani.+ 11  Ndiyeno madzi anamiza adani awo,+ Moti panalibe ngakhale mmodzi amene anapulumuka.+ 12  Pamenepo anakhulupirira mawu ake,+ Ndipo anayamba kumuimbira nyimbo zomutamanda.+ 13  Koma mofulumira anaiwala ntchito zake,+ Iwo sanayembekezere malangizo ake.+ 14  Anasonyeza chikhumbo chawo chadyera m’chipululu,+ Ndipo anayesa Mulungu m’chipululumo.+ 15  Mulungu anawapatsa zimene anali kupempha,+ Ndipo anawagwetsera matenda a kaliwondewonde pakati pawo.+ 16  Iwo anayamba kuchitira Mose kaduka mumsasa,+ Ndiponso Aroni, woyera wa Yehova.+ 17  Pamenepo dziko lapansi linatseguka ndipo linameza Datani,+ Ndi kufotsera msonkhano wa Abiramu.+ 18  Moto unayaka pakati pa msonkhano wawo.+ Malawi amoto ananyeketsa anthu oipawo.+ 19  Iwo anapanganso mwana wa ng’ombe ku Horebe,+ Ndipo anaweramira chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula.+ 20  Choncho anasinthanitsa ulemerero wanga+ Ndi chifaniziro cha ng’ombe yamphongo yodya udzu.+ 21  Iwo anaiwala Mulungu, Mpulumutsi wawo,+ Amene anachita zinthu zazikulu ku Iguputo,+ 22  Amene anachita zodabwitsa m’dziko la Hamu,+ Amene anachita zochititsa mantha pa Nyanja Yofiira.+ 23  Iye anangotsala pang’ono kulamula kuti awawononge,+ Koma Mose wosankhidwa wake, Anaima pamalo ogumuka pamaso pa Mulungu,+ Ndi kubweza mkwiyo wake kuti usawawononge.+ 24  Iwo anayamba kunyansidwa ndi dziko losiririka,+ Ndipo analibe chikhulupiriro m’mawu ake.+ 25  Anapitiriza kung’ung’udza m’mahema awo,+ Moti sanamvere mawu a Yehova.+ 26  Choncho Mulungu anawalumbirira atakweza dzanja lake,+ Kuti adzawapha m’chipululu,+ 27  Ndiponso kuti adzachititsa ana awo kuphedwa ndi mitundu ina,+ Ndi kuti adzawamwaza m’mayiko osiyanasiyana.+ 28  Iwo anayamba kulambira Baala wa ku Peori,+ Ndi kudya nsembe zoperekedwa ku zinthu zakufa.+ 29  Pamene anali kukhumudwitsa Mulungu chifukwa cha zochita zawo,+ Pakati pawo panagwa mliri.+ 30  Pinihasi ataimirira ndi kuchitapo kanthu,+ Mliriwo unatha. 31  Ndipo Pinihasi anaonedwa kukhala wolungama Ku mibadwomibadwo mpaka kalekale.+ 32  Kuwonjezera pamenepo, iwo anaputa mkwiyo pa madzi a ku Meriba,+ Moti Mose sizinamuyendere bwino chifukwa cha anthu amenewa.+ 33  Iwo anamukwiyitsa Ndipo Mose anayamba kulankhula mosalingalira bwino.+ 34  Iwowa sanawononge mitundu ina ya anthu,+ Mmene Yehova anawauzira.+ 35  Iwo anayamba kusakanikirana ndi mitundu ina,+ Ndi kuyamba kuphunzira zochita zawo.+ 36  Anayamba kutumikira mafano awo,+ Ndipo mafanowo anakhala msampha wawo.+ 37  Anali kupereka nsembe ana awo aamuna+ Ndi ana awo aakazi kwa ziwanda.+ 38  Choncho anali kukhetsa magazi a anthu osalakwa,+ Magazi a ana awo aamuna ndi a ana awo aakazi, Amene anawapereka nsembe kwa mafano a ku Kanani.+ Ndipo dzikolo linaipa ndi magazi amene iwo anakhetsa.+ 39  Iwo anakhala odetsedwa chifukwa cha ntchito zawo,+ Zochita zawo zinawalowetsa m’makhalidwe oipa.+ 40  Mkwiyo wa Yehova unayamba kuyakira anthu ake,+ Ndipo iye ananyansidwa ndi cholowa chake.+ 41  Mobwerezabwereza anali kuwapereka m’manja mwa anthu a mitundu ina,+ Kuti anthu odana nawo awalamulire,+ 42  Ndi kuti adani awowo awapondereze, Komanso kuti awagonjetse.+ 43  Nthawi zambiri anali kuwalanditsa,+ Koma iwo anali kumupandukira chifukwa sanali kumumvera,+ Ndipo anali kuwatsitsa chifukwa cha zolakwa zawo.+ 44  Mulungu akamva kuchonderera kwawo+ Anali kuona kuvutika kwawo.+ 45  Zikatero anali kukumbukira pangano limene anachita ndi iwo,+ Ndipo anali kuwamvera chisoni chifukwa cha kuchuluka kwa kukoma mtima kwake kosatha.+ 46  Ndipo anali kuchititsa kuti anthu onse owagwira ukapolo Awamvere chisoni.+ 47  Tipulumutseni inu Yehova Mulungu wathu,+ Tisonkhanitseni pamodzi kuchokera m’mitundu ina,+ Kuti titamande dzina lanu loyera,+ Ndi kuti tilankhule mokondwa pokutamandani.+ 48  Adalitsike Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ Kuyambira kalekale mpaka kalekale. Ndipo anthu onse anene kuti, Ame.*+ Tamandani Ya, anthu inu!+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “Zikhale momwemo!”