Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 105:1-45

105  YAMIKANI Yehova, itanani pa dzina lake,Lengezani zochita zake pakati pa mitundu ya anthu.+   Muimbireni, muimbireni nyimbo zomutamanda,Sinkhasinkhani ntchito zake zonse zodabwitsa.+   Nyadirani dzina lake loyera.Mtima wa anthu ofunafuna Yehova usangalale.+   Funafunani Yehova ndiponso mphamvu zake.+Funafunani nkhope yake nthawi zonse.   Kumbukirani ntchito zodabwitsa zimene wachita,Kumbukirani zozizwitsa zake ndi zigamulo zotuluka m’kamwa mwake,   Inu mbewu ya Abulahamu mtumiki wake,Inu ana a Yakobo, osankhidwa mwapadera.   Iye ndi Yehova Mulungu wathu.Zigamulo zake zili padziko lonse lapansi.+   Wakumbukira pangano lake mpaka kalekale,Wakumbukira lonjezo limene anapereka ku mibadwo 1,000,   Wakumbukira pangano limene anapangana ndi Abulahamu,Ndi lonjezo limene analumbira kwa Isaki,+ 10  Lonjezo limeneli analikhazikitsa monga lamulo kwa Yakobo,Monga pangano lokhalapo mpaka kalekale kwa Isiraeli, 11  Pamene anati: “Ndidzakupatsa dziko la KananiKuti likhale gawo la cholowa chako.”+ 12  Pamene ananena zimenezi, n’kuti iwo ali ochepa.N’kuti ali ochepa kwambiri komanso ali alendo m’dzikolo. 13  Iwo anapitiriza kuyendayenda pakati pa mitundu yosiyanasiyana,Anali kuchoka mu ufumu wina ndi kupita kukakhala ndi anthu a mtundu wina. 14  Mulungu sanalole kuti munthu aliyense awachitire zachinyengo,+Koma anadzudzula mafumu chifukwa cha iwo. 15  Iye anati: “Anthu inu musakhudze odzozedwa anga,+Ndipo aneneri anga musawachitire choipa chilichonse.” 16  Iye anadzetsa njala yaikulu m’dzikomo,Ndipo anathyola ndodo zonse zopachikapo mkate wozungulira woboola pakati. 17  Mulungu anatsogoza munthu kuti anthu akewo abwere pambuyo pake,Anatumiza Yosefe amene anagulitsidwa kuti akhale kapolo. 18  Kumeneko anasautsa mapazi ake ndi matangadza,Anam’manga ndi maunyolo.+ 19  Mawu a Yehova anamuyenga,+Kufikira pamene lonjezo la Mulungu linakwaniritsidwa.+ 20  Mfumu inalamula kuti amutulutse m’ndende.Wolamulira mitundu ya anthu analamula kuti Yosefe amasulidwe. 21  Anamuika kukhala mkulu woyang’anira banja lake,Komanso wolamulira chuma chake chonse. 22  Anamupatsa ulamuliro womanga kalonga aliyense wa mfumu,+Komanso kuphunzitsa zinthu za nzeru anthu achikulire. 23  Kenako Isiraeli anapita ku Iguputo,+Yakobo anakhala monga mlendo m’dziko la Hamu.+ 24  Mulungu anachititsa anthu ake kuberekana,Ndipo pang’onopang’ono anawasandutsa anthu amphamvu kuposa adani awo. 25  Analola adaniwo kusintha mitima yawo ndi kudana ndi anthu ake,Anawalola kuchitira atumiki ake zachinyengo. 26  Ndiyeno anatumiza Mose mtumiki wake,Ndi Aroni amene anamusankha. 27  Iwowa anasonyeza Aiguputo zizindikiro za Mulungu,Ndi zozizwitsa m’dziko la Hamu.+ 28  Anatumiza mdima moti kunada.Ndipo iwo sanapandukire mawu ake.+ 29  Anasandutsa madzi awo kukhala magazi,Ndipo anapha nsomba zawo. 30  M’dziko lawo munadzaza achule,Chimodzimodzinso m’zipinda za mafumu awo. 31  Analamula kuti pagwe tizilombo touluka toyamwa magazi,Komanso ntchentche zoluma m’madera awo onse. 32  Anawagwetsera matalala m’malo mwa mvula,Anawagwetseranso moto woyaka, walawilawi m’dziko lawo.+ 33  Anawononga mitengo yawo ya mpesa ndi ya mkuyu,Ndipo anakhadzula mitengo m’dziko lawo. 34  Analamula kuti pagwe dzombe,Ndipo panagwa dzombe losawerengeka la mtundu winawake. 35  Dzombelo linadya zomera zonse m’dziko lawo.Linadyanso mbewu zonse za m’munda mwawo. 36  Mulungu anapha mwana aliyense woyamba kubadwa m’dziko lawo,Chiyambi cha mphamvu zawo zonse zobereka. 37  Ndiyeno anayamba kuwatulutsa atatenga siliva ndi golide.Pakati pa mafuko ake panalibe amene anapunthwa panjira. 38  Aiguputo anasangalala pamene Aisiraeli anatuluka m’dzikolo,Pakuti anali kuwaopa kwambiri. 39  Mulungu anayala mtambo kuti uziwatchinga,Ndipo anawapatsa moto kuti uziwaunikira usiku. 40  Anapempha nyama ndipo anawapatsa zinziri,Anawadyetsa chakudya chochokera kumwamba. 41  Anatsegula thanthwe ndipo panatuluka madzi ambiri.Madziwo anayenda ngati mtsinje kudutsa m’dera lopanda madzi.+ 42  Iye anakumbukira lonjezo lake loyera limene analonjeza mtumiki wake Abulahamu. 43  Choncho Mulungu anatulutsa anthu ake m’dzikomo anthuwo akusangalala,Anatulutsa osankhidwa ake akufuula mokondwera.+ 44  Pang’onopang’ono anawapatsa mayiko a anthu a mitundu ina,Ndipo zipatso za ntchito imene mitundu ya anthu inagwira mwakhama, anazitenga kukhala zawo, 45  Anachita zimenezi kuti asunge malangizo ake,Ndi kusunga malamulo ake.+Tamandani Ya, anthu inu!+

Mawu a M'munsi