Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 104:1-35

104  Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.+ Inu Yehova Mulungu wanga, mwasonyeza kuti ndinu wamkulu koposa.+ Mwadziveka ulemu ndi ulemerero.+   Mwadzifunditsa kuwala ngati chofunda,+ Mwatambasula kumwamba ngati nsalu ya chihema.+   Inu munamanga zipinda za m’mwamba pamadzi pogwiritsa ntchito mitanda,+ Munapanga mitambo kukhala galeta lanu,+ Mumayenda pamapiko a mphepo.+   Inu mumapanga angelo anu kukhala mizimu,+ Ndipo atumiki anu kukhala moto wonyeketsa.+   Mwakhazikitsa dziko lapansi pamaziko olimba.+ Silidzagwedezeka mpaka kalekale, mpaka muyaya.+   Munalikuta ndi madzi ngati mwalikuta ndi nsalu.+ Madziwo anakwera kupitirira mapiri.+   Chifukwa cha kudzudzula kwanu, madziwo anayamba kuthawa.+ Atamva mabingu anu anayamba kuthamanga mopanikizika kwambiri,   Kupita kumalo amene munawakonzera. Mapiri anakwera,+ Zigwa zinatsika.   Munawaikira malire kuti asapitirire malirewo,+ Kuti asamizenso dziko lapansi.+ 10  Mwatsegula akasupe m’zigwa,+ Ndipo madziwo akudutsa pakati pa mapiri. 11  Akasupewo amapereka madzi kwa zilombo zonse zakutchire.+ Nthawi zonse mbidzi+ zimapha ludzu lawo mmenemo. 12  Zolengedwa zouluka m’mlengalenga zimamanga zisa zawo pafupi ndi akasupewo,+ Ndipo zimalira m’mitengo ya masamba ambiri obiriwira.+ 13  Mulungu amathirira mapiri kuchokera m’zipinda zake za m’mwamba.+ Dziko lapansi ladzaza ndi zipatso za ntchito yake.+ 14  Amameretsa msipu kuti nyama zidye,+ Ndipo amameretsa mbewu kuti anthu agwiritse ntchito.+ Amachita zimenezi kuti chakudya chituluke m’nthaka,+ 15  Komanso kuti mutuluke vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu.+ Amachita zonsezi kuti nkhope ya munthu isalale ndi mafuta,+ Komanso kuti apereke chakudya chimene chimakhutiritsa mtima wa munthu.+ 16  Mitengo ya Yehova imathiriridwa bwino, Mikungudza ya ku Lebanoni imene iye anabzala.+ 17  Mbalame zimamanga zisa zawo mmenemo.+ Dokowe nyumba yake ndiyo mitengo ya mlombwa.+ 18  M’mapiri aatali+ ndi mmene mumakhala mbuzi zakumapiri.+ Ndipo m’mapanga ndiye mothawiramo mbira.+ 19  Wapanga mwezi kuti uzisonyeza nthawi yoikidwiratu.+ Dzuwa nalo limadziwa bwino kumene limalowera.+ 20  Munapanga mdima kuti kukhale usiku.+ Nyama zonse zakutchire zimayendayenda usikuwo. 21  Mkango wamphamvu umabangula pofunafuna nyama,+ Ndiponso popempha chakudya kwa Mulungu.+ 22  Dzuwa likayamba kuwala+ zimachoka, Ndipo zimakagona m’malo awo obisalamo. 23  Munthu amapita ku ntchito zake,+ Ndipo amagwira ntchito mpaka madzulo.+ 24  Ntchito zanu ndi zochuluka, inu Yehova!+ Zonsezo munazipanga mwanzeru zanu.+ Dziko lapansi ladzaza ndi zinthu zimene munapanga.+ 25  M’nyanja yakuya iyi ndiponso yotambalala,+ Muli zinthu zoyenda zosawerengeka,+ Muli zamoyo zazikulu ndi zazing’ono zomwe.+ 26  Zombo zimayenda mmenemo.+ Ndipo Leviyatani*+ munam’panga kuti azisewera mmenemo.+ 27  Zonsezi zimayembekezera inu+ Kuti muzipatse chakudya pa nyengo yake.+ 28  Zimalandira zimene mwazipatsa.+ Mumatambasula dzanja lanu ndipo zimakhutira ndi zinthu zabwino.+ 29  Mukaphimba nkhope yanu, zimasokonezeka.+ Mukachotsa mzimu wawo, zimafa,+ Ndipo zimabwerera kufumbi.+ 30  Mukatumiza mzimu wanu zimalengedwa.+ Ndipo mumachititsa dziko kukhala latsopano. 31  Ulemerero wa Yehova udzakhalapobe mpaka kalekale.+ Yehova adzakondwera ndi ntchito zake.+ 32  Amayang’ana dziko lapansi ndipo limanjenjemera.+ Amagwira mapiri ndipo amafuka utsi.+ 33  Ndidzaimbira Yehova moyo wanga wonse.+ Ndidzaimba nyimbo zotamanda Mulungu wanga nthawi yonse ya moyo wanga.+ 34  Kulingalira za iye kukhale kosangalatsa.+ Ine ndidzakondwera mwa Yehova.+ 35  Ochimwa adzafafanizidwa padziko lapansi.+ Ndipo anthu oipa sadzakhalaponso.+ Tamanda Yehova, iwe moyo wanga. Tamandani Ya, anthu inu!*+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “ng’ona.”
Kapena kuti “Aleluya.”