Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Masalimo 103:1-22

Salimo la Davide. 103  Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.+ Chilichonse mkati mwanga, chitamande dzina lake loyera.+   Tamanda Yehova, iwe moyo wanga, Ndipo usaiwale zochita zake zonse.+   Tamanda amene akukukhululukira zolakwa zako zonse,+ Iye amene akukuchiritsa matenda ako onse.+   Tamanda amene akuwombola moyo wako kudzenje,+ Amene akukuveka kukoma mtima kosatha ndi chifundo ngati chisoti chachifumu,+   Amene akukukhutiritsa pa nthawi ya moyo wako ndi zinthu zabwino.+ Mulungu akukuchititsa kukhalabe wachinyamata ndi wamphamvu ngati chiwombankhanga.+   Yehova akuchitira chilungamo+ Ndi kuperekera zigamulo anthu amene akuchitiridwa zachinyengo.+   Anauza Mose njira zake,+ Ndipo anadziwitsa ana a Isiraeli zochita zake.+   Yehova ndi wachifundo ndi wachisomo,+ Wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha.+   Iye sadzakhalira kutiimba mlandu nthawi zonse chifukwa cha zolakwa zathu,+ Kapena kutisungira mkwiyo mpaka kalekale.+ 10  Sanatichitire mogwirizana ndi machimo athu,+ Kapena kutipatsa chilango chogwirizana ndi zolakwa zathu.+ 11  Pakuti monga mmene kumwamba kulili pamwamba kwambiri kuposa dziko lapansi,+ Kukoma mtima kwake kosatha nakonso ndi kwapamwamba kwa onse omuopa.+ 12  Monga mmene kum’mawa kwatalikirana ndi kumadzulo,+ Momwemonso, watiikira kutali zolakwa zathu.+ 13  Monga mmene bambo amasonyezera chifundo kwa ana ake,+ Yehova wasonyezanso chifundo kwa onse omuopa.+ 14  Pakuti iye akudziwa bwino mmene anatiumbira,+ Amakumbukira kuti ndife fumbi.+ 15  Masiku a moyo wa munthu ali ngati masiku a udzu wobiriwira.+ Iye amaphuka ngati mmene duwa lakutchire limaphukira.+ 16  Mphepo ikawomba limafa,+ Ndipo pamalo amene linali sipadziwikanso,+ 17  Koma Yehova adzapitiriza kusonyeza kukoma mtima kwake kosatha mpaka kalekale,+ Kwa anthu amene amamuopa.+ Ndipo adzapitiriza kusonyeza chilungamo chake kwa ana a ana awo.+ 18  Adzapitiriza kuchita zimenezi kwa anthu osunga pangano lake,+ Ndi kwa anthu okumbukira malamulo ake ndi kuwatsatira.+ 19  Yehova wakhazikitsa mpando wake wachifumu kumwamba.+ Ndipo ufumu wake ukulamulira chilichonse.+ 20  Tamandani Yehova, inu angelo+ ake amphamvu, ochita zimene wanena,+ Mwa kumvera malamulo ake.+ 21  Tamandani Yehova inu makamu ake onse,+ Inu atumiki ake onse ochita chifuniro chake.+ 22  Tamandani Yehova inu ntchito zake zonse,+ M’malo onse amene iye akulamulira.+ Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.+

Mawu a M'munsi