Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 102:1-28

Pemphero la munthu wosautsika pamene walefuka ndipo akutula nkhawa zake kwa Yehova.+ 102  Inu Yehova, imvani pemphero langa.+ Imvani kufuula kwanga kopempha thandizo.+   Musandibisire nkhope yanu pa tsiku limene ndili m’masautso aakulu.+ Tcherani khutu lanu kwa ine.+ Fulumirani kundiyankha pa tsiku limene ndikuitana.+   Pakuti masiku a moyo wanga atha ndi kuzimiririka ngati utsi,+ Ndipo mafupa anga atentha kwambiri ngati ng’anjo.+   Mtima wanga wawauka ngati udzu ndipo wauma,+ Pakuti ndilibe chilakolako chofuna kudya chakudya.+   Chifukwa cha kuusa moyo kwanga,+ Thupi langa langotsala mafupa okhaokha.+   Ndafanana ndi vuwo wam’chipululu.+ Ndakhala ngati nkhwezule yakubwinja.   Ndafika pofooka, Ndipo ndakhala ngati mbalame imene ili yokhayokha padenga.*+   Tsiku lonse adani anga amanditonza.+ Anthu ondinyoza amagwiritsa ntchito dzina langa potemberera ena.+   Pakuti ndadya phulusa ngati chakudya.+ Ndipo zakumwa zanga ndazisakaniza ndi misozi,+ 10  Chifukwa cha kudzudzula kwanu kwamphamvu ndi mkwiyo wanu.+ Inu mwandikweza  m’mwamba kuti munditaye.+ 11  Masiku a moyo wanga ali ngati chithunzithunzi chimene chimazimiririka dzuwa likalowa,+ Ndipo ndauma ngati udzu.+ 12  Koma inu Yehova, mudzakhalapobe kwamuyaya,+ Dzina lanu* lidzakhalapobe ku mibadwomibadwo.+ 13  Inu mudzanyamuka ndi kusonyeza Ziyoni chifundo,+ Pakuti imeneyi ndi nyengo yomukomera mtima, Chifukwa nthawi yoikidwiratu yakwana.+ 14  Atumiki anu akondwera ndi miyala ya mpanda wake,+ Ndipo amakomera mtima fumbi lake.+ 15  Mitundu ya anthu idzaopa dzina lanu, inu Yehova,+ Ndipo mafumu onse a padziko lapansi adzaopa ulemerero wanu.+ 16  Yehova adzamangadi Ziyoni.+ Iye ayenera kuonekera mu ulemerero wake.+ 17  Iye adzamvetsera pemphero la anthu amene alandidwa chilichonse,+ Ndipo sadzapeputsa pemphero lawo.+ 18  Zimenezi zalembedwera m’badwo wam’tsogolo.+ Ndipo anthu amene adzakhalapo m’tsogolo* adzatamanda Ya.+ 19  Iye wayang’ana pansi ali kumalo oyera, okwezeka,+ Yehova wayang’ana dziko lapansi ali kumwambako,+ 20  Kuti amve kuusa moyo kwa akaidi,+ Ndi kumasula anthu opita kukaphedwa.+ 21  Wachita izi kuti dzina la Yehova lilengezedwe m’Ziyoni,+ Ndi kuti atamandidwe mu Yerusalemu,+ 22  Pamene mitundu ya anthu idzasonkhanitsidwa pamodzi,+ Komanso maufumu, kuti atumikire Yehova.+ 23  Moyo wanga utafika pachimake, anachepetsa mphamvu zanga,+ Anafupikitsa masiku a moyo wanga.+ 24  Ine ndinati: “Inu Mulungu wanga, Musadule pakati masiku a moyo wanga.+ Mudzakhalapo ku mibadwomibadwo.+ 25  Munaika kalekale maziko a dziko lapansi,+ Ndipo kumwamba ndiko ntchito ya manja anu.+ 26  Zimenezi zidzatha, koma inu mudzakhalapobe.+ Ndipo zonsezi zidzatha ngati chovala.+ Mofanana ndi zovala zimene zatha, mudzapezerapo zina ndipo nazonso zidzatha.+ 27  Koma inu simudzasintha, ndipo mudzakhalapo kwamuyaya.+ 28  Ana a atumiki anu adzapitiriza kukhala motetezeka pamaso panu.+ Ndipo ana awo adzakhazikika pamaso panu.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “patsindwi.”
Mawu ake enieni, “chikumbutso chanu.”
Mawu ake enieni, “anthu amene adzalengedwe.”