Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 101:1-8

Nyimbo ndi Salimo la Davide. 101  Ndidzaimba za kukoma mtima kwanu kosatha ndi chiweruzo chanu.+ Inu Yehova, ndidzakuimbirani nyimbo zokutamandani.+   Ndidzachita zinthu mwanzeru m’njira yowongoka.+ Kodi inu mudzandithandiza liti?+ Ndidzayendayenda m’nyumba yanga ndi mtima wanga wosagawanika.+   Sindidzaika maso anga pa chinthu chilichonse chopanda pake.+ Ndimadana ndi zochita za opatuka pa choonadi.+ Sindilola kuti zochita zawozo zindikhudze.+   Aliyense wopotoka maganizo amachoka pamaso panga.+ Sindichita choipa chilichonse.+   Aliyense wonenera mnzake miseche,+ Ndimamukhalitsa chete.+ Sindingathe kupirira zochita za+ Aliyense wodzikweza ndi wamtima wonyada.+   Maso anga ali pa okhulupirika a padziko lapansi,+ Kuti akhale ndi ine.+ Woyenda m’njira yowongoka,+ Ndi amene adzanditumikira.+   M’nyumba yanga simudzakhala wochita chinyengo.+ Ndipo aliyense wolankhula zachinyengo sadzapitiriza kukhala+ Pamaso panga.+   M’mawa uliwonse ndidzawononga oipa onse a padziko lapansi.+ Ndidzapha ndi kuchotsa mumzinda wa Yehova anthu onse ochita zinthu zopweteka anzawo.+

Mawu a M'munsi