Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 10:1-18

ל [Laʹmedh] 10  N’chifukwa chiyani inu Yehova mukuima kutali?+ N’chifukwa chiyani mukubisala pa nthawi ya masautso?+   Modzikweza, woipa amathamangitsa wosautsika,+ Ndipo wosautsikayo amakodwa ndi maganizo amene woipa walingalira.+   Pakuti woipa amadzitamandira ndi zilakolako zake zadyera,+ Ndipo wopanga phindu lachinyengo+ amadzitamanda.נ [Nun]Iye amanyoza Yehova.+   Chifukwa cha kutukumuka mtima kwake, woipa safufuza kuti adziwe Mulungu.+ Iye amangoganiza kuti: “Kulibe Mulungu.”+   Zochita zake zimayenda bwino nthawi zonse.+ Zigamulo zanu zili pamwamba kwambiri pamene iye sangathe kuziona.+ Onse omuchitira zoipa amawanyodola.+   Mumtima mwake amanena kuti: “Sindidzagwedezeka.+ Palibe chimene chidzandichitikira ku mibadwomibadwo.”+ פ [Peʼ]   M’kamwa mwake mwadzaza matemberero, chinyengo ndi kupondereza ena.+ Pansi pa lilime lake pamatuluka mavuto ndi zopweteka ena.+   Iye amabisalira anthu pafupi ndi midzi. Amabisalira munthu wosalakwa ndi kumupha.+ ע [ʽAʹyin]Maso ake amafunafuna waumphawi.+   Amadikirira anthu pamalo obisika ngati mkango pamalo ake obisalapo.+ Amawadikirira+ kuti atenge mokakamiza munthu wosautsika. Amakulunga wosautsika mu ukonde wake ndi kumutenga mokakamiza.+ 10  Wosautsikayo amaponderezedwa, amawerama ndi chisoni, Ndipo khamu la anthu achisoni limagwera m’manja amphamvu a woipayo.+ 11  Mumtima mwake+ amanena kuti: “Mulungu waiwala zochita zanga.+ Wabisa nkhope yake.+ Ndithudi, sadzaona kalikonse.”+ ק [Qohph] 12  Nyamukani,+ inu Yehova. Inu Mulungu, tukulani dzanja lanu.+ Musaiwale anthu osautsika.+ 13  N’chifukwa chiyani woipa amanyoza Mulungu?+ Mumtima mwake amati: “Simudzandiimba mlandu.”+ ר [Rehsh] 14  Inu mwaona mavuto ndi masautso. Mumawayang’anabe kuti muchitepo kanthu.+ Waumphawi,+ mwana wamasiye,* amadziikiza m’manja mwanu. Inu mwakhala mthandizi wake.+ ש [Shin] 15  Thyolani dzanja la woipa ndi wankhanzayo.+ Fufuzani zoipa zake zonse ndi kumulanga kufikira zoipazo zitatha.+ 16  Yehova ndi Mfumu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+ Mitundu yatheratu padziko lapansi.+ ת [Taw] 17  Mudzamva kuchonderera kwa anthu ofatsa,+ inu Yehova. Mudzakonzekeretsa mitima yawo.+ Mudzatchera khutu lanu,+ 18  Kuti muweruze mwana wamasiye komanso woponderezedwa.+ Mudzatero kuti munthu wamba wochokera kufumbi asachititsenso anthu ena kunjenjemera.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”